Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/1 tsamba 28
  • Kodi Sayansi Ingatsutse Zozizwitsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Sayansi Ingatsutse Zozizwitsa?
  • Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/1 tsamba 28

Kodi Sayansi Ingatsutse Zozizwitsa?

Kodi zozizwitsa za m’Baibulo zinachitikadi? Pali ambiri, kuphatikizapo asayansi ndi atsogoleri achipembedzo, amene amayankha kuti ayi. Iwo amaganiza kuti kukhulupirira zozizwitsa kuli kwa m’nyengo yamalaulo ndikuti sayansi yamakono yatsutsa kuthekera kwa kuchitika kwake. Chifukwa chake, kalata yotsatirayi yofalitsidwa mu The Times ya ku London ndi kusainidwa ndi asayansi ambiri iyenera kulingaliridwa. Iyo imati:

“Sikuli kokhutiritsa mwanzeru kugwiritsira ntchito sayansi monga yotsutsira zozizwitsa. Kukhulupirira kuti zozizwitsa sizingachitike kuli kwakukulukulu nkhani ya chikhulupiriro mofanana ndi kukhulupirira kuti zingachitike. . . . Zozizwitsa ziri zinthu zomwe sizinachitikepo. Mosasamala kanthu za malingaliro amene angaperekedwe ndi nthanthi kapena zivumbulutso zamakono, kuli kofunika kutsimikizira kuti sayansi (monga momwe iriri yozikidwa pa kufotokoza zinthu zomwe zinachitikapo) singanene chirichonse pankhaniyi. ‘Malamulo’ ake ali kokha kulankhula mwachisawawa zokumana nazo zathu. Chikhulupiriro chimayedzamira pa maziko ena.” (Kanyenye ngwathu.) Ndithudi, palibe njira iriyonse imene sayansi yamakono ingatsutsire nkhani za zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena