Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/1 tsamba 30
  • Kulalikira ‘Chimasuko kwa Am’nsinga’ m’Brazil

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira ‘Chimasuko kwa Am’nsinga’ m’Brazil
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupemphera?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Brazil
    Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/1 tsamba 30

Lipoti la Olengeza Ufumu

Kulalikira ‘Chimasuko kwa Am’nsinga’ m’Brazil

MZIMU wa Yehova ukugwira ntchito zazikulu pa anthu ake m’Brazil pamene akulalikira mbiri yabwino ya chimasuko kwa okhala m’nsinga za chipembedzo chonyenga. (Yesaya 61:1, 2; Luka 4:18) Mu 1947 munali Mboni 648 zokha m’dzikolo. Mu 1967 chiŵerengerocho chinakwera kufika 41,548. Ndi dalitso la Yehova, kuchiyambi kwa 1991 chinafika pa chiŵerengero chapamwamba choposa pa 302,000! Zowonadi, ‘Mulungu anaikulitsa.’ (1 Akorinto 3:7) M’chaka chautumiki cha 1990 chokha, 27,068 anabatizidwa.

Chiwonjezeko choterocho chinakupangitsa kukhala kofunika kupanga dera latsopano mwezi uliwonse, ndipo Nyumba Zaufumu zatsopano 150 zinaperekedwa m’chaka chimodzi chokha. Ndiponso, ofesi yanthambi inagula nthaka ya maekala 450 kuti afutukule malo awo osindikizira, kumene tsopano akusindikiza Mabaibulo pa makina awoawo osindikizira. Chotero Mboni m’Brazil zimagwira ntchito zolimba kuthandiza ofatsa mtima kutuluka mu ‘Babulo Wamkulu’ pamene ‘chisautso chachikulu’ chisanadze.​—Chibvumbulutso 7:9, 10, 14; 18:2, 4.

□ Wofalitsa wina wazaka zisanu ndi zitatu anasiya bukhu kwa mkazi wa mkulu wa apolisi ndiyeno, ali yekha, anapanga ulendo wobwereza. Cholinga chake chinali chakuti donayo adziŵerenga zina za nkhanizo kwa iye ndikumamuuza zimene wamvetsetsa mu iriyonse. Pamene mkaziyo anafotokoza nkhanizo kwa iye, iye yekha mkaziyo anayamba kuliyamikira bukhulo nampempha kuti akamdziŵitse kwa amayi ake. Wofalitsayo anatero, ndipo tsopano donayo akusangalala ndi phunziro Labaibulo lapanyumba lokhazikika.

□ Mu 1984, Maria anatopa nacho chinyengo chimene ankawona m’chitaganya, ndipo anathedwa nzeru chifukwa cha ngozi zimene ankaziŵerenga zimene zinkachitika m’dziko. Choncho anayamba njira ya moyo yosonyeza mzimu wachipanduko. Iye akuti: “Chonulirapo chathu chinali kuchita motsutsana ndi chirichonse ndi aliyense. Mawonekedwe anga anali kokha ndi cholinga chakudabwitsa anthu​—kuwoneka wosiyana ndi ena, zovala za mtundu wakuda, mutu wometedwa mbali imodzi. Ndinanyalanyaza mwamuna wanga, ana, ndi nyumba ndipo ndinayamba kusuta marijuana ndi kugwiritsira ntchito cocaine kotero kuti ndiiŵale zochitika zenizeni za m’moyo. Komatu izi zinandipangitsa kumva moipirapo. Ndinkalira. Pamene ndinaŵerenga Baibulo, sindinkamvetsetsa. Chotero ndinapemphera kwa Mulungu kaamba ka chithandizo.

“Tsiku lina Mboni ziŵiri zinafika panyumba panga, pambuyo pa kukambitsirana kwachidule, zinandigaŵira magazini aŵiri. Potembenuza masamba a imodzi ya iwo, ndinawona nkhani ya mutu wakuti ‘Kusadalira pa Mulungu​—Kulekeranji?’a Nkhaniyo inandikhudza mtima. Ndinalingalira kuti Mulungu adayankha mapemphero anga, ndipo tsiku lomwelo, Mbonizo zinayamba kuphunzira nane Baibulo. Kuchokera pamenepo kumkabe mtsogolo ndinapanga masinthidwe akukhala munthu wabwinopo. Mwamuna wanga ndi banja poyamba anatsutsa kuphunzira kwanga Baibulo, koma pamene anawona masinthidwe amene ndinkapanga, anayamba kundilimbikitsa. Tsopano ndine mtumiki wobatizidwa wa Yehova.”

Mboni za Yehova m’Brazil, mofanana ndi m’mbali zonse za dziko lapansi, nzokangalika m’kulalikira ‘chimasuko kwa am’nsinga.’ Makamu akuvomereza, namapeza chimasuko chenicheni ndi chimwemwe muutumiki wa Yehova.

[Mawu a M’munsi]

a Kope la Nsanja ya Olonda ya March 15, 1986.

[Bokosi patsamba 30]

BRAZIL

Chiŵe. cha Anthu - 150,367,800

Chiŵe. Chapa. cha Ofali. mu 1990 - 293,466

Kugaŵa, Wofalitsa 1 pa - 512

Chiŵe. cha Obati. mu 1990 - 27,068

Avar. ya Ofali. Achipainiya - 30,115

Chiŵe. cha Mipingo - 4,625

Avar. ya Maphu. Abaibulo - 341,305

Opezeka pa Chikumbutso - 790,926

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena