Lipoti la Olengeza Ufumu
Yehova Apereka Thandizo
POSACHEDWAPA, Mboni za Yehova mu South Africa zinalandira mawu onena za tsoka lothetsa nzeru la abale awo auzimu okhala m’dziko lapafupi komwe ntchito yawo yolalikira njoletsedwa. Iwo anauzidwa kuti chifukwa cha chilala chachikulu, abale awo ankapulumuka mwakudya mizu ina. Iwo analibenso zovala zoyenera, chimene chinapangitsa Mboni zina kukhala zankhokera kukhala ndi phande muuminisitala wakumunda.
Abale aku South Africa anachitapo kanthu mofulumira. Pempho linaperekedwa ku mipingo yakumaloko m’dera la Johannesburg ponena za kufunika kwa zovala. M’masiku ochepa okha, matani atatu a zovala anaperekedwa. Zinthuzo zinasankhidwa ndi antchito odzipereka mwaufulu. Makonzedwe anapangidwa akutumiza matani 3 a nyemba, tani imodzi ya mafuta, tani imodzi ya sopo, ndi matani 17 a ufa wachimanga. Pamene kampani imene inapereka ufa wachimangawo inamva za tsoka la Mboni zokhala m’dziko lokanthidwa ndi chilala, inatumiza chakudya chofunika kwambirichi choposa tani imodzi monga chopereka.
Pa Lolemba, April 16, 1990, galimoto yaikulu yokhala ndi katundu wa matani 25 a zinthu zofunikirazo inanyamuka ku South Africa kunka pa ulendo wake wa makilomita 5,500. Komano panafunikira chilolezo kuchokera kwa olamulira kuti atenge katunduyo kudutsa m’dziko lawo lokanthidwa ndi nkhondo.
Olamulira okhala pa ofesi ya kazembe m’dzikolo ananena kuti chinkana kuti Mboni za Yehova sizimazindikiridwa m’dziko lawo, iwo amadziŵa za kukhalapo kwawo. Sipakakhala chowaletsa kukapereka zinthu zothandizazo kwa abale athu. Chilolezo chinaperekedwa. Zikalata zoyenerera zinaperekedwa, ndipo pa Lachisanu, April 20, Mbonizo zinaoloka malire popanda vuto. Komabe, anapeza maroadblock oposa 30, pamene anafunikira kusonyeza zikalata zawo. Pamenepo mpamene anazindikira kufunika kwa zikalatazo.
Atayenda kwa mtunda wa makilomita 140 kuloŵa m’dzikolo, anatsekerezedwa ndi mtsinje waukulu wosefukira. Ulalo woyamba unawonongeka, ndipo wongoyembekezera womwe unalipowo unali wosayenerera kaamba ka galimoto yaikuluyo. Komabe, anapeza kuti galimoto yaing’ono yomwe inali pagulu la apaulendolo ikanatha kuoloka ulalo wosefukirawo mosavuta. Anasankhapo kugawana magulu aŵiri. Msasa unamangidwa pa mtsinje wosefukirawo kaamba ka gulu limodzi, pamene gulu linalo linapitiriza ulendo wake kukakumana ndi abale chakumpoto mtunda wa makilomita 260 owonjezereka. Iwo anali achimwemwe chotani nanga pamene pomalizira pake anakumana ndi abalewo! Iwo sanaleke kumwetulira, kukumbatirana, ndi kugwirana chanza. Posakhalitsa magalimoto aakulu aŵiri akumaloko ananyamuka kukachingamira gulu lina la abale omwe ankadikirira pamtsinjewo. Kumeneko, zinthu zothandizazo zinasamutsidwa kuchoka m’galimoto yaikuluyo kunka m’magalimoto aŵiri aang’onowo.
Malipoti olandiridwa akusonyeza chiyamikiro chakuya kaamba ka thandizo la Yehova la zinthu zakuthupi. Komabe, mosasamala kanthu za tsoka lawo lakuthupi, abalewo analirira kwenikweni chakudya chauzimu. Mpingo wina unkalandira kope limodzi lokha la Nsanja ya Olonda, lomwe linakopedwa kaamba ka banja lirilonse. Chiyamikiro chinke kwa Yehova, popeza kuti makonzedwe apangidwa tsopano akupereka mokhazikika chakudya chauzimu kwa abale okhala m’dzikolo.