‘Phanga la Achifwamba’ Lamakono
M’MAGAZINI a Natural History, profesa wa anthu ndi miyambo yawo Colin Turnbull anasimba zokumana nazo zake monga mlendo wocheza ku Yerusalemu. Iye anati “mzimu wa Krisimasi” umene anayamba kukhala nawo “unaphedwa mofulumira” pamene anawona masitolo a mzinda ali “phaphapha ndi zinthu zosafunika kwenikweni zikugulitsidwa pamtengo wodabwitsa kwa ogula za Krisimasi (alendo) omwe adawonekera kukhala otengeka ndi maganizo ofunitsitsa kugula.”
Turnbull adati ponena za “mzimu [wake] wa Krisimasi”: “[Uwo] unafoketsedwa mowonjezereka ndiri pamalo ena omwe ndidaganiza kuti angaulimbitsenso [uwo]—malo a Manda Oyera.” (Mkati mwake mowonekera pamwambapa.) Kumeneko, mkhalidwe wa alendo anzanga “omwe anawonekera kusonyeza kupanda ulemu kotheratu kaamba ka chopatulikacho” unamlefulitsa pamene iwo “ankakankha ndikumaloŵa mwanjira yosakhala Yachikristu kwenikweni, akumagwiritsira ntchito mapeŵa ndi zigongono kumaloŵa mokankha ndimphamvu pakhomo lopapatiza la mandawo. Nthaŵi ndi nthaŵi panabuka kumenyana pang’ono, kotsagana ndi kutukwana ndi majesichala zosemphana kotheratu ndi kupatulika.”
Mmalo mwa “kusunga mkhalidwe wa kupatulika,” Turnbull anati, atsogoleri achipembedzo oyang’anira “anachotsapo lingaliro lirilonse la chiyero mwakupereka chitsanzo iwo eni cha mkhalidwe wa ndewu.” Iye anasimba za “wina wowonekera kukhala Mkulu Wachipembedzo, wovala mkanjo wofiira modera, ndi woopsa” yemwe “mwamphamvu anakankhira kumbuyo alendo wamba kuwachotsa pakhomo pa mandawo nthaŵi iriyonse pamene gulu la alendo achuma (otchedwa pilgrims), okhala ndi makandulo anabwera, atatsogozedwa ndi Mkulu Wachipembedzo wina.” Mphunzitsiyo anati, chotulukapo chake chinali “nkhalwe pakati pa osanyamula makandulo ndi onyamula makandulo, limodzinso ndi pakati pa akuluakulu achipembedzo osiyanasiyana, popeza kuti panawoneka kukhala kuloŵana m’malo kosatha kwa magulu achipembedzo audani akumapikisanira nthaŵi ndi malo.”
Mnzake wa profesa Turnbull adali “[mamita] angapo patali kumbuyo kwa kachisiyo, atagwada napinda manja ake, akuwoneka pang’ono mkati mwa chibowo m’khoma.” Turnbull anasimba kuti: “Pamene ndinkawonerera, dzanja lake lamanja linatuluka nilipapasa m’thumba mwake kufuna ndalama, koma mkono wake winawo unatsalabe mkatimo, utatambasulidwa monga ngati kuti unagwidwa. Komabe, ataloŵetsa ndalamayo m’chibowomo, mkono wake wakumanzere unataidwa ndipo bwenzi langa linanyamuka . . . M’dzanja lake lakumanzere anagwira kamtanda kathabwa kakang’ono, konyowa mmene kanawazidwa madzi onenedwa kukhala oyera ndi mwamuna wachipembedzo yemwe adachita kugulitsako nabisalanso mkati mwa phanga laling’ono, akumayembekezera mnkhole wake.”
Yesu Kristu anawona kachitidwe kofananako kwa anthu otchuka pa kachisi, ndipo anawauza kuti anali kumtembenuza kukhala ‘phanga la achifwamba.’ (Luka 19:45, 46) Ndithudi, m’tsiku lathu ‘mapanga a achifwamba’ oterowo sali ku Yerusalemu kokha.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.