Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 12/1 tsamba 31
  • “Misozi Yachiyamikiro”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Misozi Yachiyamikiro”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 12/1 tsamba 31

“Misozi Yachiyamikiro”

“NDIKULIRA misozi yachiyamikiro, ndangomaliza kumene kuŵerenga nkhani yakuti ‘Mmene Mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe.’” (Nsanja ya Olonda ya March 15, 1990, masamba 26-30) Mmenemo ndimo inayambira imodzi ya makalata ambiri olandiridwa ndi Sosaite oyamikira nkhani zonena za kuchita tondovi zotuluka m’makope athu a March 1 ndi March 15, 1990. Komabe, mawu enieni awa anachokera kwa mlongo wa ku Japan amene posachedwapa mwana wake wamwamuna wam’ng’ono anakanthidwa ndi matenda a kusokonezeka maganizo. Iye akulongosola motere:

“Nthaŵi zina, ndimatopa n’kutonthoza ndi kulimbikitsa munthu wochita tondovi tsiku lirilonse. Pamene kwada, mwana wanga wamwamuna amagwidwa ndi mantha ndi kuda nkhaŵa. Choncho ndimampatsa mankhwala ogonetsa ndikukhala pambali pa kama wake kumasisita manja ndi mphumi yake kufikira atagona. Nkofanana ndi kugoneka khanda, ndipo pambuyo pa pafupifupi ola limodzi, iye amagona tulo tofanato. Pamenepo mpamene ndimadzimva womasuka, komabe panthaŵi imodzimodziyo, ndimadziuza kuti m’mawa mmamawa udzabweretsa tsiku lina lofunikira kupirira nazo.

“Mwana wangayo amati, ‘Ndine wopanda pake. Palibe chiyembekezo chirichonse kwa ine.’ Tsiku lirilonse amafunsa momvetsa chisoni kuti, ‘Kodi matenda angaŵa adzachiritsidwa? Kodi ndidzamasuka liti ku mankhwala? Kodi moyo umenewu udzakhalako kwautali wotani?’ Panthaŵi zoterozo ndimagwiritsira ntchito mafunso kusintha kuganiza kwake monga mmene magaziniwo anaperekera lingaliro, ndipo ichi chimamthandiza kupezako bwino. Komabe timapyola m’zimenezo tsiku ndi tsiku.

“Pamakhalanso nthaŵi zimene mwana wanga amaitana akulu [a mumpingo wathu] pakati pausiku pamene akudzimva wodera nkhaŵa kwenikweni ndikuwapempha kuti ampempherere. Ichi chimawoneka kukhala chotonthoza kwambiri kwa iye ndikupumulitsa maganizo ake. . . . Nthaŵi zambiri, mkhalidwe wa mwana wanga umafika poipa pamene mwamuna wanga (wosakhulupirira) achokapo pamaulendo abizinesi. Pamene ndipempha thandizo palamya, abale ambiri amathamangira kunyumba kwathu.

“Ndikuthokozani, abalenu, kuchokera pansi pa mtima chifukwa chofalitsa nkhani za mtundu uwu kwa nthaŵi ndi nthaŵi ndikusonyeza kwanu kuti mumasamalira zosoŵa za ofooka.”

[Yosainidwa] H. H.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena