“Tsopano Tiri ndi Nyumba Yaufumu Yathu Yathu”
ZAMBIRI zafalitsidwa ponena za Nyumba Zaufumu zomangidwa mofulumira m’maiko onga Great Britain, Canada, ndi United States. Komabe, chosadziŵika kwambiri ndicho nsonga yakuti malo olambirira omangidwa mofulumira a Mboni za Yehova akhala akumangidwa kwa zana makumi angapo m’maiko otchedwa otukuka kumene.
M’maiko a mu Afirika Mboni zakumaloko kaŵirikaŵiri zimamanga misasa yosakhalitsa m’milungu yoŵerengeka yokha kaamba ka misonkhano yachigawo. Imeneyi yatumikira osati kokha monga malo osokhanira ndi kuchinjirizidwa ku dzuŵa lotentha komanso monga malo ogona kaamba ka nthumwi. Zokumana nazo zofananazo zingasimbidwe ponena za Central America.
Mwachitsanzo, mu Mzinda wa Guatemala, mu Guatemala, chopereka cha $200 chinatumizidwa ku Mpingo wa Mboni za Yehova wa Vivibien. Pamene Mboni yakumaloko inapereka puloti la dziko ku malo akumudzi, Mbonizo zinasankha kugwiritsira ntchito choperekacho kumanga nyumba yodekha imene ikagwiritsiridwa ntchito kaamba ka misonkhano yawo.
Nsungwi zinafunikira kumangira chochinga chautali wa mita imodzi ndi theka; pamwamba nkusiya malo oloŵetsa mphepo. Iwo anafuna kuti chimangocho chikhale cha ukulu wa mamita 4 muufupi ndi 6 muutali. Pamene akulu ampingowo anayendera malowo, anadabwa kupeza minda ya nsungwi patsogolo pa pulotilo, zautali wochokera pa mamita 6 mpaka 9 ndi ukulu wa masentimita 8 kufika ku 13. ‘Bwanji sitiimanga pa Loŵeruka lotsatira?’ iwo anatero.
Usiku wotsatira Lachitatu, mapulani omangira anapangidwa. Lachinayi mbale wina anagula malata ofolerera, wina matabwa, ndi winanso misomali. Pofika Lachinayi masana matabwawo anadulidwiratu mu ukulu wofunika, ndipo anayamba kupanga nsanamira zonga A za zitsulo zoperekedwa. Pofika Lachisanu usiku nsanamirazo zinatha.
Loŵeruka m’mamawa, lole inapereka nsanamirazo ndi matabwa ena, malata, ndi misomali ku mudziko. Magalimoto anayi anapereka kumudzi anthu chifupifupi 50, amuna, akazi ndi ana. Pofika 8:00 a.m. onse anafika.
Mizati inakumbiridwa pa mwala wolimba. Nthaŵi yapita Mbonizo zinagula nsungwi zokwanira 50 kwa mwini mundawo wa nsungwi pa 12 cents imodzi—chiwonkhetso cha $6. Mwamsanga, analikha nsungwizo ndi zisenga. Zinadulidwa mu utali wa mita imodzi ndi theka ndi kung’ambidwa pakati.
Pamene nsanamirazo zinali kuikidwa, ena anali kukhomerera nsungwi zong’ambidwazo moimika ku nzengo zopingasa, theka limodzi kunja ndi linalo mkati, kotero kuti mbali youlungika mosalala ya nsungwizo ikakongoletsa ponse paŵiri zipupa zamkati ndi zakunja. Chotsatira, denga linaikidwa pamene ena anayamba kubweretsa miyala ndi dothi kuti asalaze pansi. Kusanade nyumba ya maola 12 imeneyo inamalizidwa, ndipo abale anabwerera kunyumba zawo mu mzinda ndi mitima yokondwa.
Pambuyo pake, masamba a mlaza anayalidwa pansi padothipo, ndipo mipando yothyola ndi mabenchi ena opangidwa ndi nsungwi zosagwiritsiridwa ntchito anaikidwa. Tsopano Nyumba Yaufumuyo inali yokonzeka kaamba ka msonkhano woyamba.
M’maiko ambiri a m’malo otentha—Afirika, Pacific ndi zisumbu za Caribbean, Asia, Mexico, Central ndi South America—kumene mwina mamiliyoni a Mboni za Yehova amakhalako, nyumba zosavuta zoterozo zadzetsa chisangalalo kwa Mboni za kumaloko chifukwa chakuti anakhoza kunena kuti: “Tsopano tiri ndi Nyumba Yaufumu yathu yathu.”