Pamene Imfa Itenga Wokondedwa
“MU 1981 amayi anga anamwalira ndi kansa. Anali amayi anga opeza. Imfa yawo inali yovutitsa kwa ine ndi mlongo wanga wopeza. Ndinali ndi zaka 17, ndipo mlongo wanga anali ndi zaka 11. Ndinawalakalakadi amayi kwambiri. Ndinaleredwa monga Mkatolika, ndipo pokhala nditaphunzitsidwa kuti anali kumwamba, ayi, ndinafuna kudzipha kotero kuti ndikakhale nawo. Adali bwenzi langa lapamtima.”—Roberta, zaka 25 zakubadwa.
Kodi munayamba mwakhalapo ndi chokumana nacho chofananacho? Ngati ndi tero, mukudziŵa bwino lomwe kupweteka kumene kumatsagana ndi kutayika kwa wokondedwa. Zimawoneka kukhala zoipa kuti imfa iri ndi mphamvu yotenga winawake amene mumamkonda. Ndipo pamene zimenezo zichitika, lingaliro la kusakhalanso wokhoza kulankhulana, kuseka naye, kapena kugwira wokondedwa wanu lingakhale lovuta kwambiri kulipirira. Ndipo monga mmene mawu a Roberta akusonyezera, kupweteka kumeneko sikumachotsedwa mwakuuzidwa kuti wokondedwa wanu ali kumwamba.
Komabe, kodi ndimotani mmene mungamverere mutadziŵa kuti nzotheka kudzagwirizananso ndi wokondedwa wanu womwalira nthaŵi yakutsogolo posachedwapa, ayi, osati kumwamba koma pompano pa dziko lapansi pansi pa mikhalidwe yamtendere, yolungama? Ndipo kodi bwanji ngati mutadziŵanso kuti pa nthaŵi imeneyo anthu adzakhala ndi chiyembekezo chosangalala ndi umoyo wangwiro ndipo kuti sadzafanso? ‘Ndithudi kulingalira kopeka!’ mungatero.
Komabe, kalelo m’zaka za zana loyamba C.E., Yesu Kristu ananena molimbika mtima kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:25) Limenelo linali lonjezo lakuti akufa adzakhalanso ndi moyo—chiyembekezo chosangalatsadi!
Komabe, mwinamwake mukuzizwa kuti: ‘Kodi pali maziko odalirika okhulupirira lonjezo limenelo? Kodi ndingatsimikize motani kuti sikungolingalira kopeka? Ndipo ngati pali maziko okhulupirira zimenezo, kodi kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli kungatanthauzenji kwa ine ndi okondedwa anga?’ Nkhani yotsatira idzalongosola mafunso ameneŵa ndi ena.