Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/1 tsamba 32
  • Chochitika Chimene Simuyenera Kuphonya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chochitika Chimene Simuyenera Kuphonya
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/1 tsamba 32

Chochitika Chimene Simuyenera Kuphonya

“Chitani ichi chikumbukiro changa.” Mawu amenewa a Ambuye wathu Yesu Kristu, opezeka pa Luka 22:19, ananenedwa panthaŵi imene anakhazikitsa chikumbutso cha imfa yake. Inali imfa ya Yesu imene inatsegulira anthu chiyembekezo cha kupeza moyo wosatha mumkhalidwe wa paradaiso. Chotero imfa yake ndiyo kanthu kena kamene tiyenera kukumbukira.

Kodi mudzapezeka pachikumbutso cha chaka chino?

Chonde landirani chiitano ichi kuchokera kwa Mboni za Yehova kukagwirizana nazo pokumbukira chochitika chofunikachi. Chochitikachi chidzakhalako pambuyo pakuloŵa kwa dzuwa pa deti limene limalingana ndi Nisani 14 panyengo ya kalenda ya Baibulo. Lembani chizindikiro padetilo pakalenda yanu kotero kuti musaiŵale. Iyo idzakhala April 10, 1990. Mboni za Yehova za kwanuko zingakuwuzeni malo ndi nthaŵi yeniyeni pamene chochitikachi chidzakhalako kwanuko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena