Kodi Nchifukwa Ninji Yehova Wavumbula Dzina Lake?
Ndemanga ina ya “Chipangano Chakale” yofalitsidwa m’Poland mu 1964 inayankha funso limeneli mwanjira yodzutsa maganizo kwambiri. Mololezedwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika, Dr. Stanisław Łach, profesala pa Yunivesite ya Lublin, anati:
“Anthu owomboledwa ali ndi thayo lodziŵitsa dzina la Mulungu pamaso pa anthu.” Linali thayo la Aisrayeli kupanga kuyesayesa kotero “kuti akunja adalitse dzina la Yahwe [Yehova] kuti asalinyoze.” “Yahwe liri ndi tanthauzo . . . Dziko lidzaŵeruzidwa modalira pakachitidwe kawo kulinga kwa awo amene amavomereza dzina limenelo.” Profesalayo analengeza kuti “Dzina lakuti Yahwe lidzakhala lalikuru pakati pa amitundu . . . Lidzafalikira padziko lonse lapansi. Chimenecho chinali choikidwiratu cha . . . dzinalo kwa Mose.”
Inde, monga momwe Malaki 1:11 akuloselera: “Dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wamakamu.” Ndipo kodi ndani lerolino amene akulengeza dzina limenelo padziko lonse lapansi kotero kuti “yense amene akaitana padzina la Yehova adzapulumutsidwa”? Mboni za Yehova! Kulabadira kwa anthu onse kwa “anthu a dzina lake” ameneŵa, inde, “onse ovomereza dzina limenelo,” ndiko nkhani ya moyo ndi imfa kwa iwo. Kodi inu mukulabadira motani kwa Yehova ndi Mboni zake?—Machitidwe 2:21; 15:14; yerekezerani ndi Malaki 3:16-18.