Chizunzo Chipitirizabe mu Burundi
KUCHIYAMBI kwa 1989, olamulira a mtundu wa pakati pa Africa wa Burundi anayambitsa mkuntho wa chizunzo pa Mboni za Yehova. Monga mmene zinasimbidwira m’kope la Nsanja ya Olonda ya August 15, 1989, olamulirawo anayesera kukakamiza Mbonizo kuleka chikhulupiriro chawo, kugwiritsira ntchito kuvutitsa, kumangidwa, kumenyedwa, ndi miyezo ina yopweteka. Kodi mkhalidwe wakhala wotani chiyambire pa nthaŵiyo?
Ripoti lina lochokera m’Burundi likunena kuti mkati mwa kuchezera kwa woyang’anira wachigawo ku Kinyinya ndi Gitega, olamulira anayesera kumanga ziŵalo za mpingowo pa msonkhanopo. Woyang’anira wachigawo ndi wadera anathaŵa, koma awo amene anamangidwa anaphatizikapo ophunzira pa sukulu yapamwamba aŵiri ndi msungwana wa ku sukulu ya pulaimale. Onsewo anamenyedwa. Tsiku lotsatira Mboni zimene zinamangidwa zinawonekera pamaso pa bwanamkubwa ndi kulongosola chifukwa chimene sizikanakhalira ziŵalo za chipani cha ndale zadziko. Iwo anamenyedwanso. Maripoti ena akusimba za zinthu zofananazo.
Mkulu Wachikristu wathayo mu Burundi akulemba kuti: “Palibe Mboni ya Yehova imene yamangidwa chifukwa cha kuba, kupha, kapena kuwukira. Ngati olamulira anali ndi zifukwa zenizeni za kulangira Mboni, lolani kuti atero m’bwalo lamilandu lapoyera m’malo mozunza nzika zamtendere, kulanda katundu wawo, ndi kuwathamangitsa ngati nyama zakuthengo. Abale ambiri mkati mwa dzikolo akakamizika kuthaŵa m’nyumba zawo ndi kukhala ngati othaŵathaŵa. Mlongo wina amene mwamuna wake ali m’ndende wapita kukawonana ndi olamulira kwa nthaŵi zambiri kuyesera kuti mwamuna wake amasulidwe. Iye wabwezedwa ndi onse ndi yankho lakuti: ‘Sitingamasule konse mwamuna wako pamene iwe ukupitiriza kulandira ndalama kuchokera kunja kotero kuti musokoneze mtendere m’dziko lathu.’ Ndi kusinjirira kotani nanga!”
Komabe, pali mbiri yabwino yochokera m’Burundi. Mbonizo sizikuwopa kapena kulefulidwa. Mochenjera koma motsimikizirika kulalikira kwa mbiri yabwino kukufutukuka, ndipo abale ndi alongo akuzindikira kuti mwachidaliro chotheratu mwa Yehova, iwo angapirire. Makalata ambiri osonyeza kusakondwa alembedwa kale kupita ku Burundi, ndipo mosakaikira ena ambiri adzatsatira pamene dziko lidzadziŵa kuti Burundi akupitirizabe ndawala yake yopanda chifundo ya kuzunza Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 15]
Adresi ya presidenti wa ku Burundi ndi:
His Excellency Major Pierre Buyoya
President of the Republic of Burundi
Bujumbura
REPUBLIC OF BURUNDI