Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 11/1 tsamba 5
  • “Kuyankha Mowongoka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kuyankha Mowongoka”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Yendani ‘M’njira Yoongoka’
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kugwiritsa Ntchito Baibulo Popereka Mayankho
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Akulu, Weruzani Mwachilungamo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • ‘Madalitso Ali pa Wolungama’
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 11/1 tsamba 5

“Kuyankha Mowongoka”

MU ULALIKI wa pa Phiri, Yesu analozera ku “chilamulo ndi aneneri.” Mbali yachitatu ya Malemba Achihebri inali Zolembedwa, zimene zinaphatikizapo mabukhu a ndakatulo, onga ngati Masalmo ndi Miyambo. (Mateyu 7:12; Luka 24:44) Awanso, anali ndi nzeru ya Mulungu.

Mwachitsanzo, miyamboyo inachenjeza oweruza mu Israyeli wakale kuti: “Wonena kwa woipa, wolungama iwe; magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira. Omwe amdzudzula adzasekera, nadzadalitsika ndithu. [Woyankha mowongoka, NW] apsompsona milomo.”​—Miyambo 24:24-26.

Ngati woweruza anagonjera ku zididikizo za chiphuphu kapena wako ndi wako ndi kulengeza woipa kukhala wolungama, ena akamuwona iye kukhala wosayenera malo ake. Nkulekeranji, popeza kuti ngakhaledi ziŵalo za Amitundu “magulu a mitundu” omwe anamva za kupotozedwa kwa chiweruzo koteroko ankaipidwa! Ku mbali ina, ngati woweruza molimba mtima anadzudzula munthu woipa ndi kumyankha mowongoka pa mlandu wozengedwawo, iye akapeza ulemu ndi kukondedwa ndi anthuwo. Anthu onsewo akafulumizidwa kumfunira iye “madalitso abwino.” Monga momwe mwambiwo ukuchiikira mowonjezereka kuti: “[Woyankha mowongoka, NW] apsompsona milomo.”

Kupsompsona koteroko kunatanthauza kulemekezana​—pakati pa phungu ndi awo olabadira chidzudzulo chake chowongoka. Mwinamwake ngakhale yemwe akudzudzulidwa akachitapo kanthu moyanja ndi kusonyeza kukonda kwake woweruzayo. Miyambo 28:23 ikutero kuti: “Adzamkomera mtima wodzudzula mtsogolo mwake, koposa wosyasyalika ndi lilime lake.” Chotero awo otumikira monga akulu a mpingo lerolino ayenera kupeŵa kulola ubwenzi kapena unansi wa banja kuipitsa chiweruzo chawo. Mwa kupereka uphungu wofunikira mowongoka, akulu adzapeza ulemu mu mpingo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena