Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/1 tsamba 31
  • Aids—‘Kodi Nkuyamba kwa Makhalidwe Abwino Atsopano’?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aids—‘Kodi Nkuyamba kwa Makhalidwe Abwino Atsopano’?
  • Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/1 tsamba 31

Aids​—‘Kodi Nkuyamba kwa Makhalidwe Abwino Atsopano’?

ATATCHULA kuti dokotala wamankhwala ananena kuti “kugonana ndi mnzanu mmodzi yekha” ndiyo njira yokha yopeŵera kutenga AIDS mwakugonana, wolemba nkhani ya mkonzi wa magazine wa ku Canada akufunsa kuti: “Kodi AIDS yowopsyayo ingakhale kuyamba kwa makhalidwe abwino atsopano m’dziko lathu?” Mkonziyo anadabwanso, kuti kaya ngati sikuli “kwachilendo” kuti chimene Baibulo laphunzitsa kwa zaka zambiri, kutanthauza, kukhala ndi wokwatirana naye mmodzi, “tsopano chingakhale populumukira pa anthu.” Posonyanso ku dziko lamakonoli la “anam’goneka, fodya, zakumwa zoledzeretsa ndiponso kwakukulukulu, kumwerekera m’zakugonana,” nkhani ya mkonziyo ikuti: “Tsopano tikulipirira kuwononga dziko ndi zithunzi zosonyeza umaliseche, kusasankha m’zakugonana kumene takupanga.”

Pamene kuli kwabwino kuyembekezera kuwongokera m’kudzisungira ndiponso kuti tikhalabe ndi moyo, kodi ndiko kokha kuwopa kufa msanga kapena mapeto a mtundu wa anthu kumene kudzabweretsa “makhalidwe abwino atsopano kotheratu”? Ayi, chifukwa chakuti mosasamala kanthu za machenjezo ochokera kwa adokotala ndi ofufuza, osuta fodya ambiri ndi achigona m’baŵa akupitirizabe mopusa kuipitsa thanzi lawo, kuithetsa miyoyo yawo mofulumirirapo. Ndipo ogonana a ziŵalo zofanana ena anena kuti adzapitirizabe kukhala ndi ogonana nawo ochuluka ngakhale pali upandu wa kutenga AIDS.​—Miyambo 10:21, 23.

Pamenepa, kodi nchiyani chimene chidzatetezera kuchita zoipa mowona mtima? Ndithudi, mantha abwino ndi kuchitira ulemu Yehova, zowoneka mwa kumvera malamulo ake onena za makhalidwe abwino. “Kuwopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziŵa.” Ndipo mtundu wachidziŵitso chimenechi umapereka nzeru imene ndithudi “isunga moyo wa eni ake.”​—Miyambo 1:7; Mlaliki 7:12.

Mofunikira, mkonziyo, powona kuti AIDS ingapatsiridwe kupyolera mwa kuthiridwa mwazi, anafunsanso kuti: “Kodi [sikuli] koseketsa kuti ife amene tatsutsa kotheratu Mboni [za] Yehova chifukwa cha kukana kuthiridwa mwazi . . . tsopano tifunikira kuchita chinthu chimodzimodzicho kaamba ka zifukwa zina?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena