Kupandukira Makhalidwe a Zakugonana—Kale ndi Makono
KODI ndimotani mmene kulambira Moleke, mmodzi wa milungu ya Chimoabu kunaliri konyansa? Paolo Mantegazza akulemba m’bukhu lake lakuti The Sexual Relations of Mankind kuti Amoabu a m’nthaŵi za Baibulo anaseŵera machitachita a zakugonana “m’nyimbo, pamene ankavina mozugulira fano loyaka moto la Moloki, pambuyo pakuti pakamwa pa mkuwa pasanu ndi paŵiri pa mulunguyo panali patadya nsembe za okhulupirika, nsembe zomwe zinaphatikizapo ufa wa tirigu, njiŵa, ana a nkhosa, nkhosa zamphongo, ana a ng’ombe, ng’ombe zamphongo, ndi ana ang’ono aamuna.” Iye akuwonjezera kuti: “Aliyense yemwe waŵerenga Baibulo ayenera kukumbukira matemberero owopsya operekedwa ndi Mose pa Ahebri amenewo omwe anachita chisembwere ndi Moloki. Baal-Phegor, nayenso, kapena Belphegor [Baala wa ku Peori], yemwe anali mulungu wokondeka wa Am[i]diyani, analandiridwa ndi chikondwerero chopanda maziko ndi Ayuda, ndipo zikhulupiriro zake zinali zoipa mofanana ndi miyambo ya Moloki.”—Levitiko 18:21, New World Translation Reference Bible, mawu a m’munsi; 20:2-5; Numeri 25:1-5; Yeremiya 32:35.
“Chikondwerero chopanda maziko” cha Ayuda amenewo chimapeza kufanana kwake lerolino mu “makhalidwe atsopano” amene anawonekera, makamaka mu United States ndi maiko ena a Chikristu cha Dziko, mu ma 1960.
M’kupenda ziyambukiro zonka patali za kusintha kwa zakugonana kumeneko, Adokotala Alexandra ndi Vernon H. Mark, akonzi a bukhu lakuti The Pied Pipers of Sex, anapereka malingaliro awo m’chigawo chotchedwa “Speaking Out” cha Medical World News, Houston, Texas, U.S.A. Mu 1985 iwo analemba kuti:
“Pa zaka 25 zapita, chitaganya chachitira umboni kusintha kwakukulu m’makhalidwe a zakugonana. . . . Kusintha kumeneku kwa makhalidwe a mwambo kwatchedwa kusintha kwa kugonana.” Pambuyo potchula aprofesa a zamankhwala omwe ali ndi thayo kaamba ka kusintha kumeneku m’kachitidwe ka kugonana, alembiwo analengeza kuti: “Chifukwa cha ukulu wa kuthandizira kwawo kwaumwini, [a zamakhwala amenewa] akhala ndi chiyambukiro chodabwitsa pa chitaganya ndi makhazikitsidwe ake onse. M’malo mopereka chiyamikiro kwa olinganiza zakugonana amenewa, ife tifunikira kuthetsa chisonkhezero chawo mwa kupititsa patsogolo kawonedwe kokhazikika ndi kolinganizika kulinga ku kachitidwe ka kugonana ndi chitetezero chaumoyo wa anthu.
“Kuperekedwa kwa kudidikiza kokwanira kwa kusintha kwa zakugonana sikunatulutse nkomwe mapindu aliwonse ku dziko lonse—pokhapo titalingalira ponena za phindu la ndalama. Koma ndi chigogomezero chake pa kugonana monga chosangulutsa ndi maseŵera openyereredwa, chisinthikocho chatulutsa unyinji wa mavuto omwe akutiwopsyeza ife ndi tsoka la mayanjano—nthenda yopatsirana mwa kugonana kukhala imodzi ya iwo. VD siiri vuto latsopano, koma iyo tsopano yakhala mliri, ikumayambitsa mitundu yatsopano ya tizirombo tachilendo ta bacteria ndi tizirombo tina tothandizira tosawoneka ndi maso. Matuza a kumpheto, osachiritsika mwa akulu, achititsa imfa za makanda zochititsidwa ndi meningoencephalitis (matenda a ubongo). AIDS . . . yaloŵa m’chitaganya chathu ndi m’mitsempha ya mwazi ya minkhole yopanda liwongo kupyolera m’mwazi woipitsidwa wosonkhedwa.”
Alembi amenewa akumaliza kuti: “Umboni womakulakula wosuliza atsogoleri a kusintha kwa kugonana uli wosangalatsa. Iwo analonjeza chisangalalo, chimasuko, ndi umoyo wabwino. Iwo apereka tsoka, nthenda, ndipo ngakhale imfa.” Baibulo limamveketsa bwino pamene atsogoleri oterewa akuima. Mwachitsanzo, 1 Akorinto 6:9, 10 ikunena kuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasokeretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudzipsya ndi amuna . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”—Onaninso Yuda 7.