Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 9/1 tsamba 10
  • ‘Zofunika Zifika’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Zofunika Zifika’
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Zinthu “Zofunika” Zikudzaza Nyumba ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Onse Alemekeze Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Ine Ndili Nanu”
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 9/1 tsamba 10

Ripoti la Olengeza Ufumu

‘Zofunika Zifika’

MNENERI Hagai analemba mawu awa mu 520 B.C.E.: “Ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:7) “Zofunika” za amitundu onse zomwe zadzaza nyumba ya Yehova ndi ulemerero ziri alambiri ake owopa Mulungu. Anthu owona mtima oterowo akuvomereza ku mbiri yabwino mu Italy, kotero kuti tsopano kuli Mboni 166,000 zikuphunzitsa anthu Baibulo m’dzikolo. Atsogoleri achipembedzo Achikatolika mu Italy akulingalira kukula kwathu kwapadera kukhala “kuwonjezereka kochitika mowopsya” kumene “kukuwadetsa nkhaŵa ndi kuwathetsa nzeru” iwo. Lolani wofunafuna chowonadi wina kumeneko asimbe chimene chinachitika kwa iye.

“Ndinali mphunzitsi wa Akatolika osabatizidwa kwa zaka khumi, ndipo ndinakhutiritsidwa kuti iyi inali njira yolongosolera chikondi changa kaamba ka Mulungu ndi mnansi. Ngakhale kuti ndinali ndi bwenzi yemwe anali mmodzi wa Mboni za Yehova, sindinawombolepo nthaŵi kumvetsera ku uthenga wa Baibulo. Ngakhale kuli tero, nthaŵi ina kumbuyo, pamene Mboni zinandifikira, ndinaziitanira mnyumba. Ndinafuna kuwauza kuti asachezere apongozi anga kachiŵirinso, popeza kuti anali kudzimva ozunguzika. ‘M’malo mochezera anthu achikulire,’ ndinawawuza iwo, ‘lankhulani kwa anthu onga ine.’ Kuchokera pamenepo iwo anabwera mokhazikika ku nyumba yanga, koma nthaŵi iriyonse pamene iwo anakhudza pa nsonga ya chiphunzitso, ndinkawapempha iwo kulekeza kukambitsiranako kufikira nthaŵi ina mtsogolo kotero kuti ndikafufuze nkhaniyo.

“Ndinalankhula kwa ansembe osiyanasiyana ndi kuzindikira kuti iwo analibe yankho la Baibulo. Mmodzi wa iwo, m’mishonale, anandiwuza ine kuti sichinali chofunikira kwenikweni kupezeka pa Misa. ‘Ndiko nkomwe,’ iye anatero kuti, ‘m’maiko onga Brazil, mwachitsanzo, anthu amachita zinthu zina m’malo mopita ku Misa. Chinthu chofunika kwambiri chiri kutumikira Mulungu bwino koposa monga mmene wina angathere.’ Mawu amenewa anandipatsa nyonga ya kudula zomangira zanga ndi Tchalitchi cha Chikatolika. Wansembe wina anawuza mwamuna wanga, yemwe analinso m’Katolika, kuti ngati ndinafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, iye andilole ine kutero chifukwa chakuti Mboni za Yehova ziri ndi cholakwa chimodzi chokha, chija cha kukhala zachangu mopambanitsa. Ndinabatizika posachedwapa limodzi ndi mmodzi wa ana anga aamuna. Mwamuna wanga akuphunziranso Baibulo ndipo akusonyeza chikondwerero mu uthenga wa Ufumu.”

Pamene Yehova akugwedeza mitundu mwa kulola ziweruzo zake kulengezedwa pa dziko lapansi, anthu ambiri amaganizo ayedzamira ku chilungamo akusiya machitachita osawona mtima kotero kuti atsatire maprinsipulo a Baibulo. Asanaphunzire chowonadi, mwamuna wina wa ku Italy analoŵa m’ngongole zochulukira, akumaganiza kuti akakhoza kubwezera ngongole yake ndi ndalama zochokera m’malipiro ake okhazikika ndi “mapindu” osawona mtima omwe iye anali kulandira. Atapeza chidziŵitso cha chowonadi, iye anapanga chigamulo chovuta ndi kuleka kulandira “mapindu” osawona mtima. Iye ndi mkazi wake anabatizidwa ndipo mosataya nthaŵi anayamba kutumikira mu utumiki wa nthaŵi zonse. M’chipatala mmene akugwira ntchito, iye kaŵirikaŵiri amafunikira kuvula mitembo, ndipo mobwerezabwereza wapeza ndalama zochulukira pa iyo. Mwachitsanzo, nthaŵi ina anapeza 150,000 lire (chifupifupi $115, U.S.), ndipo nthaŵi inanso 600,000 lire (chifupifupi $460, U.S.). Pokhala wowona mtima, iye anabweza ndalamazo, ndipo ichi chinampatsa mwaŵi wa kulankhula kwa oyang’anira a chipatala ndi adokotala ponena za chowonadi. Oyang’anira a chipatala anamutumizira makalata a chiyamikiro kaamba ka kuwona mtima kwake ndi kachitidwe ka thayo.

Zokumana nazo zimenezi kuchokera ku Italy ziri kokha chitsanzo cha mmene “zinthu zofunika” zikusiira dongosolo iri loipa, lachiwawa ndi kubwera ku gulu la Yehova loyera, lamtendere iye potsirizira pake asanagwedeze dongosolo la Satana la ndale zadziko m’chiwonongeko pa Armagedo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena