‘Chilangizo Chenicheni cha Mkhalidwe’
Mtsikana wa msinkhu wa zaka 14 wa ku Nigeria, West Africa, ali woyamikira kulandira chilangizo choterocho kuchokera m’bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It. Iye akulemba kuti:
“Bukhu limeneli liri lothandiza koposa, lowonadi, lodabwitsa ndipo ntchito ya luso yokondweretsa. Ilo mowonadi lidzakhala la chithandizo chachikulu kwa aliyense amene ali woyedzamira ku kukhala wotsogozedwa mwamtendere kupyola zinthu zonse zoipa za m’moyo.
“Ndadziŵikitsa bukhu limeneli kwa anzanga a ku sukulu ndi anansi. Aliyense yemwe amaliŵerenga ilo amayamikira zisonyezero zanu ‘zomangirira nzeru’ ndi nkhani zokambitsiridwa m’bukhulo. Tikulingalira kuti nsonga zosonyezedwa m’bukhulo sizidzawunikira kokha kapena kupereka nzeru ndi kufuna maprinsipulo a mkhalidwe odekha, koma zingapereke zitsogozo zabwino kwa achichepere ndi achikulire omwe akufuna kusangalala ndi mtendere weniweni wa maganizo ndi umoyo, ndi omwe angachite kudziletsa kwaumwini ndi kusonyeza mphamvu kaamba ka chimene chiri choyenera. . . .
“Kumaliza nkhani yonseyo, bukhu limeneli liri lomvekera bwino ndi lodzaza ndi chilangizo chenicheni cha mkhalidwe wa zakugonana chomwe sichingapezedwe kwa makolo ambiri kapena aphunzitsi . . . Mmene ndikukhumbira kuti bukhulo likanadziŵitsidwa ku sukulu kaamba ka maphunziro a tsiku ndi tsiku a m’kalasi, ndi lingaliro la kukhazikitsa mkhalidwe wa moyo wa mtendere, wokondeka, wobala zipatso ndipo wa tanthauzo.”
Bukhu lakuti Your Youth—Getting the Best out of It limayankha mafunso oterowo onga ngati, Nchifukwa ninji achichepere ayenera kuphunzira mu sukulu? Ndimotani mmene ayenera kuwonera makolo awo? Kodi iwo ayenera kukhala ndi unansi wa kugonana asanakwatire? Kodi iwo ayenera kumwa zakumwa zoledzeretsa? Landirani kope kaamba ka kokha K10 mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 192 Your Youth—Getting the Best out of It. Ndatsekeramo K10 (Zambia).