Kodi Kuwopa Kuli Koipa Nthaŵi Zonse?
IKO kungasakaze chimwemwe ndi kuwononga chiyembekezo. Iko kwalozeredwa kukhala ululu wa maganizo, wowononga wa lingaliro, ndipo kwanenedwa kukhala kowononga kwenikweni kuposa nthenda yakuthupi yoipitsitsa. Inde, kuwopa kuli mkhalidwe wa maganizo wamphamvu. Komabe, kodi kuli koipa nthaŵi zonse?
Tangolingalirani kuti inu mukuyendetsa galimoto mu msewu wosazoloŵereka. Msewuwo ukukwera m’mapiri ndi kuyamba kukhotakhota ndi kutembenuka. Usiku uyamba kufika, ndipo limodzi nawo kubwera fumbi loyera la mame a chipale chofewa. Galimoto yanu itsetsereka pang’ono, ndipo inu muzindikira kuti mwafika pa malo okwezeka pamene msewuwo uyamba kukutidwa ndi madzi owundana.
Tsopano muyenera kukhala amaso kwambiri. Pamene inu mukuyesa mosamalitsa kutembenuza galimoto yanu pa malo okhota aliwonse okutidwa ndi madzi owundana, muzindikira mmene chikakhalira chopepuka kulephera kutembenuza galimoto pa malo otererawo ndi kugwera m’chigwa pansipo. Kuwonjezerapo, inu mulibe lingaliro la ngozi zina zomwe zikukuyembekezerani mu mdimawo. Pamene malingaliro onga awa abwera ku maganizo, milomo yanu imawuma ndipo mtima wanu umagunda mofulumira pang’ono. Inu muli ogalamuka kwenikweni. Mosasamala kanthu za chirichonse chomwe munali kulingalira papitapo, inu tsopano muli odzazidwa kotheratu ndi ntchito yomwe muli nayo: kusunga galimoto kukhalabe pa msewu ndi kupeŵa ngozi.
Pomalizira, msewuwo utsikira ku malo a kunsi. Kuli magetsi a mkhwalala, ndipo kulibenso madzi owundana. Mwapang’onopang’ono, kumangika kuchoka m’thupi lanu. Inu mumasuka ndi kupuma mpweya wampumulo. Kuwopa konseko kunangodza pachabe!
Koma kodi konseko kunangodza pachabe? Osati kwenikweni. Kunjenjemera kolingalirika pansi pa mikhalidwe yoteroyo kuli kuyankha kwa thupi kwachibadwa. Kumatipangitsa ife kukhala amaso, ochenjera. Kuwopa kwabwino kungatithandize kusachita chirichonse mofulumira, kudzivulaza ife eni. Inde, kuwopa sikuli nthaŵi zonse wowononga wa lingaliro kapena ululu wa maganizo. Pansi pa mikhalidwe ina, iko kungathe ngakhale kukhala kopindulitsa.
Baibulo limalankhula ponena za kuwopa ndipo limabweretsa mitundu iŵiri yapadera ku chisamaliro chathu. Mtundu umodzi wa kuwopa uli ndithudi ululu wa maganizo. Koma winawo suli kokha wachibadwa ndipo wabwino koma wofunikira ku chipulumutso chathu. Kodi ndi iti yomwe iri mitundu iŵiri ya kuwopa? Ndipo ndimotani mmene ife tingaphunzirire kukulitsa kumodziko ndi kupeŵa kwinako? Chimenechi chidzakambitsiridwa m’nkhani yotsatira.