Chiwiya Chofufuzira Chaphindu
“Ndikuyamikani kaamba ka zofalitsidwa zanu za mavolyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!,” akulemba tero wa msinkhu wa zaka 13 wa ku New Zealand. Mtsikanayo akulongosola kuti:
“Mphunzitsi wanga anafunsa kalasi kuchita kufufuza pa tsoka lirilonse ndipo kenaka kuika ilo mu mtundu wa kabukhu. Ndinasankha kuphunzira ponena za Titanic. Ndinafunafuna kaamba ka mabukhu pa sukulu koma sindinapeze lirilonse loyenera. Chotero ndinayang‘ana mu volyumu ya Galamukani! (m’Chingelezi) ya ‘81. Ndinawerenga nkhani yonse yonena za Titanic, ndipo kenaka m’mawu anga, ndinaika iyo mu mtundu wa kabukhu. Pamene mphunzitsi wanga anachonga ntchito zonse, iye anasonyeza yanga ku kalasi. Ndinapambana onse.” Wachichepereyo akumaliza kuti: “Nthaŵi iriyonse pamene ndikhala ndi ntchito, ndidzagwiritsira zofalitsidwa zanu.”
Mwakupeza mabound volyumu a magazini iyi, nanunso mudzakhala ndi chiwiya chofufuzira chaphindu. Bound volyumu ya Galamukani! (Chingelezi) ya 1988 tsopano iripo, limodzinso ndi bound volyumu ya Nsanja ya Olonda (Chignelezi), magazini inzake ya Galamukani! Landirani mavolyumu anu mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chongani kabokosi kalikonse, kapena tonse tiŵiri, ndi kutumiza chopereka choyenera. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)
[ ] Chonde tumizani bound volyumu ya Galamukani! (Chingelezi) ya 1988. Ndatsekeramo K60 (Zambia).
[ ] Chonde tumizani bound volyumu ya Nsanja ya Olonda (Chingelezi) ya 1988. Ndatsekeramo K60 (Zambia).