Chochitika Chofunikira Kukumbukira!
PANALI pa Nisani 14 ya chaka cha 33 C.E.
Yesu ankagawana chikho cha vinyo ndi mtanda wa mkate wopanda chotupitsa ndi atumwi ake. Malangizo ake? “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Chotero kamodzi pa chaka, Mboni za Yehova kuzungulira dziko zimakumana pamodzi kukumbukira imfa ya Yesu m’njira imene iye analangizira pa usiku umene iye anapanga ndemanga imeneyo. Chaka chino, Nisani 14 idzayamba pa Lachitatu, March 22, pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa. Inu mukuitanidwa mothentha kudzagwirizana nafe mu msonkhano wokumbukira umenewu pa madzulo a Lachitatu limenelo. Chonde fufuzani ndi Mboni za Yehova za kumaloko kaamba ka nthaŵi yotsimikizirika ndi malo a kukumanako.