Mawu a Chikhulupiriro Kuchokera ku Ndende ya Imfa
Pa January 6, 1940, wachichepere wa ku Austria Franz Reiter analembera mayi wake kuchokera ku malo otsekeredwa a Nazi mwamsanga kuphedwa kwake kusanakhale: “Kukhala kuno, ndingasinthebe maganizo anga, koma ndi Mulungu ichi chikakhala kusakhulupirika. . . . Ndi chimene ndikudziŵa, ngati ndikanatenga lumbiro [la nkhondo], ndikanapanga chimo loyenerera imfa.”
Ngati munayang’anizana ndi imfa, kodi mukanapotoza maprinsipulo amene mumadziŵa kukhala olondola? Anthu a ku Austria ambiri anakana kugonjera. Iwo analibe mbali m’chipani cha ndale zadziko cha Hitler kapena mikangano ya nkhondo. Ena anafa m’misasa yake ya chibalo. Limbikitsani chigamulo chanu chenicheni mwa kuŵerenga mbiri yodzetsa nthumanzi ya umphumphu wa Akristu a ku Austria kumayambiriro ndi mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II.
Ndiponso ŵerengani maripoti osangalatsa ponena za ntchito ya Mboni za Yehova mu Barbados ndi Ecuador, limodzinso ndi chithunzi cha pa nthaŵi ino cha ntchito ya dziko lonse. Zonsezo ziri mu 1989 Yearbook of Jehovah’s Witnesses.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, 1989 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Ndatsekeramo K8 (Zambia).
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
DÖW, Vienna, Austria