Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 12/15 tsamba 30
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Chirimikani Molimbana Ndi Machenjera a Satana
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kupulumutsa Bukhu la Makedzana la Sinaiticus
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 12/15 tsamba 30

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwapereka kulingalira kosamalitsa ku makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati ndi tero, inu mwinamwake mudzakhala okhoza kukumbukira zotsatirazi:

◻ Nchiyani chomwe chiri magwero a chimwemwe chowona?

Yesu ananena kuti: “Odala iwo akumva mawu a Mulungu nawasunga!” (Luka 11:28) Chotero Yesu anasonyeza kuti chimwemwe chowona chimapezedwa m’kukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ndi kuchita chifuno chake.​—8/15 , tsamba 8.

◻ Ndi iti yomwe iri njira imodzi imene tingatsutsire machitachita a Satana ochenjera ndi achinyengo?

Kuti titsutse Satana, tiyenera kudzisanthula ife eni. Kodi tiri ndi chifooka chimene Satana angadyerere kapena akuchidyerera tsopano lino? Mwachitsanzo: Kodi tiri ndi vuto la malingaliro? Kodi nthaŵi zonse tifunikira kukhala oyambirira? Ngati timadzidziŵa ife eni, chotero tingawongolere mavuto oterowo, malinga ngati tiri odzichepetsa. Mwanjira imeneyi, sitidzadzisiya ife eni otseguka kwa Satann.​—9/1, masamba 15, 16.

◻ Nchiyani chomwe chiri chizindikiro chophiphiritsira chimene ‘mwamuna wovala bafuta’ wophiphiritsirayo akuika pa awo omwe amakhala “nkhosa zina” za Kristu? (Ezekieli 9:2-4; Yohane 10:16)

“Chizindikiro” chiri umboni wakuti onga nkhosa oterowo ali odzipereka, anthu obatizidwa okhala ndi umunthu wonga wa Kristu.​—9/15, tsamba 14.

◻ Nchiyani chimene mtumwi Petro anatanthauza pamene ananena kuti tiyenera “kukondana wina ndi mnzake kwenikweni kuchokera ku mtima”? (1 Petro 1:22)

“Kwenikweni” m’chenicheni kumatanthauza “mofutukuka.” Kaamba ka chikondi choterocho kuti chisonyezedwe pakati pa Akristu chimafunikira kuyesetsa ndi kutambasula mitima yathu kotero kuti ingakute anthu kwa amene mwachibadwa sitingakokedwereko.​—10/1, tsamba 12.

◻ Nchiyani chomwe chiri kachisi woloseredwa pa Chibvumbulutso 11:1, ndipo ndi liti pamene anakhalako?

Ali kachisi wauzimu wokulira, mwa amene mopatulikitsa ali malo okhalako a Yehova m’mwamba. Anakhalako mu 29 C.E. pamene Yesu anadzozedwa ndi kuyamba kutumikira monga mkulu wa nsembe. (Ahebri 3:1; 10:5)​—10/15, tsamba 12.

◻ Nchiyani chomwe chiri Bukhu la Makedzana la Sinaiticus, ndipo kodi ilo liri lofunika chotani?

Bukhu la Makedzana la sinaiticus liri ndi Malemba a Chikristu a chigriki onse ndi matembenuzidwe a Chigriki a mbali za Malemba a Chihebri. Ilo liri chifupifupi zaka 1,600, ndipo limapanga kugwirizanitsa kofunika mu ndandanda yathu ya mamanusikripiti a Baibulo.​—10/15, masamba 30, 31.

◻ Nchiyani chomwe chimapangitsa chimwemwe chachikulu koposa mu ukwati?

Wokwatira aliyense ayenera kutsimikizira kuti Mulungu ali mu ukwati wawo. Mwa njira imeneyi, zosowa zauzimu zidzakwaniritsidwa, ndipo chomangira cha ukwati chidzalimbikitsidwa. (Mlaliki 4:12; Mateyu 5:3)​—11/1, tsamba 16.

◻ Nchiyani chomwe chiri “mtendere wa Mulungu” umene mtumwi Paulo akulankhula ponena za iwo pa Afilipi 4:7?

Mtendere umenewu uli bata ndi kudekha kopatsidwa ndi Mulungu, ngakhale pakati pa mikhalidwe yoyesa koposa. Iwo umatulukapo kuchokera ku unansi wathithithi ndi Yehova ndi chitsimikiziro chakuti chimene wina akuchita chiri chokondweretsa m’maso mwake.​—11/1, tsamba 30.

◻ Ndi kupyolera mwa chiyani mmene wina amakhala wovomerezedwa ndi Yehova?

Kupyolera m’kudzipereka ndi kubatizidwa, chiri chothekera kwa munthu wopanda ungwiro kukhala ‘munthu wokondwera naye,’ kapena munthu wovomerezedwa ndi Mulungu. (Luka 2:14)​—11/15, tsamba 11.

◻ Nchiyani chomwe makolo angachite kuthandiza ana awo ang’ono olakwa ngakhale ngati iwo sanayeneretsedwe monga wofalitsa wosabatizidwa kapena ngati iye ali wochotsedwa?

Mongadi mmene makolo adzapitirizira kupereka chakudya, zovala, ndi pogona, choteronso amafunikira kulangiza ndi kulanga iye m’chigwirizano ndi Mawu a Mulungu. Iwo angaphunzire ndi iye yekha kapena kukhala ndi iye akugawanamo mu makonzedwe a phunziro la banja.​—11/15, tsamba 20.

◻ Ndimotani mmene mwambo Wachiyuda unasiyanirana ndi lamulo la Mulungu pa Eksodo 20:12 kuti ana ayenera kulemekeza makolo awo?

Munthu akanaika chikole katundu wake kuti adzaperekedwe pambuyo pake ku kachisi mwa kulengeza kuti anali “korban,” chomwe chinatanthauza, “mphatso yoperekedwa kwa Mulungu.” (Marko 7:11) Korban ameneyo akagwiritsiridwabe ntchito ndi munthuyo ku phindu lake, koma akanakaniza iyo kwa makolo ake.​—12/1, masamba 4, 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena