Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 12/1 tsamba 32
  • Nkhani Zimene Ana Amakonda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani Zimene Ana Amakonda
  • Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1988
w88 12/1 tsamba 32

Nkhani Zimene Ana Amakonda

CHAKA chatha malikulu a Watch Tower Society mu Brooklyn analandira kalata yotsatirayi kuchokera ku Sherwood, Oregon:

“Mabwana:

“Posachedwapa ndinatenga bukhu kuchokera mu laibulale lokhala ndi mutu wakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kaamba ka ana anga a zaka 4 ndi 6 zakubadwa. Nkhanizo zinakambidwa m’njira imene iwo angathe kumvetsetsa, ndipo iwo asangalala mokwanira kuŵerenga nkhani za Baibulo. Tingakonde kuwonjezera bukhuli ku laibulale yathu yaumwini.

“Kumbuyo kwa bukhulo kunanena kuti kope lingapezedwe mwa kulembera keyalayi ndi kutumiza K1.70. Bukhulo likuwoneka ngati kuti lakhala likusindikizidwa kwa nthaŵi yaitali. Kodi mungandiuze ine mtengo wa pa nthaŵi ino kotero kuti ndingatumize ndalamazo ndi kulandira bukhulo?”

Pa kutulutsidwa kwake mu 1978, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo linali K1.70, koma tsopano chopereka chiri K24. Inunso mungalandire kope lochitiridwda chitsanzo mokongolali, la zirembo zazikulu, chofalitsidwa cha masamba 256 mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi K24.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K24 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena