Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 11/1 tsamba 7
  • Kupirira kwa Mwamuna Kugwirizanitsa Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupirira kwa Mwamuna Kugwirizanitsa Banja
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Otsimikiza Mtima Kutumikira Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Mboni za Yehova Zimathetsa Maukwati a Anthu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 11/1 tsamba 7

Ripoti la Olengeza Ufumu

Kupirira kwa Mwamuna Kugwirizanitsa Banja

NCHIYANI chimene mungachite ngati munalandira chowonadi ndipo kenaka mnzanu wa mu ukwati mwaukali atsutsa inu ndi kuchita chirichonse cha mu mphamvu yake kuswa umphumphu wanu? Kodi mukalimbikitsidwa ndi mawu a Paulo pa 2 Timoteo 3:12, NW kumene iye akunena kuti: “Iwo onse okhumba kukhala ndi moyo wodzipereka kwaumulungu m’chigwirizano ndi Kristu Yesu adzazunzidwanso”? Kodi inu mukapirira kapena mukagonjera? Mwamuna Wachikristu mu Italy anakumanizana ndi chitokoso choterocho. Iye sanagonjere, ndipo Yehova anamudalitsa iye kaamba ka icho.

Mwamuna wokambidwayo kumbuyoko anali mkomyunizimu wokangalika, koma iye analinso m’Katolika wachangu. Iye anakhulupirira m’kulingana kwa anthu ndipo anadzimva kuti zipani ziŵiri zonsezo zinalalikira lingaliro limeneli. Mmodzi wa ogwira nawo ntchito ake analankhula kwa iye ponena za Ufumu wa Mulungu, ndipo iye panthaŵi yomweyo anazindikira kuti iyi inali njira yokha yomwe kulingana kungafikiridwire. Iye anatenga chowonadi ndi kutenthedwa maganizo kofananako komwe iye anasonyeza kaamba ka chikomyunizimu ndi Chikatolika ndipo anabatizidwa mu 1972. Bwanji ponena za mkazi wake? Iye mwaukali anamutsutsa. Mkaziyo akulongosola kuti:

“Munali mu 1970 pamene mwamuna wanga anali ndi kugwirizana kwake koyamba ndi Mboni za Yehova pa malo ake a ntchito. Mwapang’onopang’ono, pamene iye anaphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti chinali chipembedzo chatsopano ndipo chinali ndi nsonga zomwe sindinagwirizane nazo. Chizunzo chinayamba mwamsanga kuchokera kwa ine ndi ziwalo zina za banja.”

Iye akupitiriza: “Makolo a mwamuna wanga anamusautsa iye, kugwiritsira ntchito njira iriyonse yothekera kumletsa iye. Pamene mwamuna wanga anapita patsogolo m’chidziŵitso cha Baibulo, iye anawona kufunika kwa kuchotsa mafano m’nyumba yathu. Ndinamuuza iye kuti ngati iye akachita chimenecho, chinachake choipitsitsa chikachitika. Iye anawononga chithunzi cha chipembedzo, ndipo ndinayambitsa kuwukira kotheratu kwa mawu ndi kwakuthupi pa iye ndi kung’amba ochulukira a magazini ake. Pa kufuula kwanga, apongozi anga anathamangira mkati ndi kudziponyanso iwo eni pa iye, koma iye sanabwezere.

“Kusamvanako kunapitiriza kufikira ndinamusiya iye pamene iye anatsutsa mwana wathu wamkazi kupezeka pa katekizimu ku tchalitchi. Mwamuna wanga anandiuza kuti ngati sindinabwerere kunyumba, iye akayambitsa mlandu wa kuthaŵa. Patapita mlungu umodzi ndinalingalira kubwerera.

“M’kuyesera kowonjezereka kwa kumuimitsa iye, ndinapita kwa wowombeza maula ndi kufunsa kuti amulodze iye. Wa maulayo anayamba kundifunsa, ndipo ndinalongosola mkhalidwewo. Pamene anamva iwo, iye anandiuza ine kuti palibe mtundu wa malodza womwe uli ndi chiyambukiro chirichonse pa mmodzi wa Mboni za Yehova.

“Tinalingalira za kufikira wansembe wa kumaloko. Wansembeyo anatilangiza ife kupita kwa loya. Ku kudabwitsidwa kwanga loyayo anandilimbikitsa ine kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova ndi mwamuna wanga. Apongozi anga a amuna, omwe anali ndi ine, anatsutsa, akumanena kuti banja lawo linali lodzipereka kotheratu kwa San Rocco, ‘Mtetezi’ wa mzinda wathu. Ngakhale kuli tero, loyayo analongosola kuti ‘woyera’ ameneyu, monfanana ndi mafano ena onse, anali wonyenga. Kenaka iye anadzizindikiritsa iyemwini monga tcheyamani wa Kachitidwe ka Chikatolika ndi kutiuza ife kuti iye sanatenge mbali nkomwe m’mapwando onse a chipembedzo chifukwa, pokhala ataŵerenga Baibulo, iye anadziŵa kuti iwo onse anali onyenga. M’kumaliza, iye ananena kuti: ‘Pita ndi mwamuna wako ndipo khala pa mtendere. Mvetsera kwa iye, ndipo iwenso uyambe kukphunzira Baibulo.’

“Ndi chilimbikitso chimenechi, ndinawunikira pa mkhalidwe, masinthidwe, ndi kupirira kwa mwamuna wanga, ndipo ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova limodzi ndi iye. Wokondweretsedwa ndi chikondi chosonyezedwa kumeneko, ndinaphunzira, kulembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki, ndi kuyamba mu utumiki wa m’munda. Potsirizira pake, ndinachitira chizindikiro kudzipereka kwanga mu 1977 ndipo ndiri wachimwemwe tsopano kukhala m’chowonadi, chiyamikiro chipite kwa Yehova yemwe anathandiza mwamuna wanga kupirira ndi kugwirizanitsa banja lonse m’kulambira Kwake.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena