Kuyang’ana pa Grisi
Nzika zoyambirira zondziŵika za Grisi zinkatchedwa Ionians. Chikukhulupiridwa kuti dzina limeneli linachokera ku kholo lawo lakale Javan (Chihebri, Ya·wanʹ), mwana wa Yafeti ndipo chotero mdzukulu wa Nowa. (Genesis 10: 1, 2) M’malemba a Chikristu a Chigriki a Baibulo, Grisi amatchedwa Hel·lasʹ. Liri dziko losasalala ndi la miyala, ndi mapiri odzaza ndi mitengo. Nthaŵi yaitali kumbuyoko Agriki anakhala akatswiri aluso a m’nyanja.
Agriki akale anali ndi milungu yambiri, yolongosoledwa monga yokhala ndi mkhalidwe waumunthu ndi kukongola kokulira. Milungu imeneyi molingaliridwa inadya, kumwa, ndi kugona; ndipo ngakhale kuti inalingaliridwa kukhala yoyera ndi yosafa, iyo inayenganso ndi kugwirira chigololo ndipo inali yokhoza kunama ndi upandu. Nthanthi zoterozo zingakhale m’chenicheni zikumbukiro zopotozedwa za nthaŵi ya Chigumula chisanakhale pamene ana a amuna aungelo a Mulungu mowukira anadza ku dziko lapansi, nagonana ndi akazi, nabala mbadwa zamphamvu zotchedwa Anefili, ndi kudzaza dziko lapansi ndi chiwawa.—Genesis 6:1-8, 13.
M’zana lachinayi B.C.E., Philip wa ku Macedon, atate wa Alexander Wamkulu, anakhazikitsa ponena za kugwirizanitsa mzinda wakale wa dziko la Grisi lidziimira pa lokha, kuubweretsa iwo pansi pa kulamulira kwa Makedoniya. M’zana lachiŵiri B.C.E., Grisi inakhala dera la Roma, ndipo mwambo wa Chigriki unafalikira ku Roma.
Kugwiritsira ntchito kofala kwa koi·neʹ ya Chigriki kunathandizira ku kukula kwa mwamsanga kwa mbiri yabwino ya Chikristu kupyola mu dera la Mediterranean.
Mtumwi Paulo anachezera Makedoniya ndi Grisi mkati mwa maulendo ake achiŵiri ndi achitatu a umishonale. Iye anapanga mipingo ya Chikristu mu Filipi, Tesalonika, Korinto, ndi Bereya. Sila, Timoteo, Tito, ndi Akristu ena oyambirira nawonso anaphunzitsa pano. Lerolino, Grisi iri ndi mipingo yoposa 320 ya Mboni za Yehova ndi kupita patsogolo kwa ofalitsa oposa 23,000 a Ufumu wa Mulungu.