Thandizo mu Kusankha Mabwenzi
Kodi mungagwiritsire ntchito lina? Achichepere amayang’anizana ndi zosankha zolemera zambiri pamene akukula m’nthaŵi zino zovuta. Mtsikana wachichepere wochokera ku Britain akulemba ponena za thandizo loperekedwa ndi Your Youth—Getting the Best out of It:
“Ndiri wotsimikizira kuti ilo liri bukhu labwino koposa lomwe linalembedwapo kaamba ka ana. Ndiri ndi zaka 13 zakubadwa, ndipo landithandiza ine ndi zinthu zambiri, zonga ngati ‘Nchifukwa Ninji Kuphunzira ku Sukulu?,’ ‘Kodi Mumamaliza Chimene Mwayamba?,’ ndi ‘Ndi Mabwenzi a Mtundu Wanji Amene Mumafuna?’ Ndinali ndi mavuto ena posankha mabwenzi, ndipo mutu umenewu wandithandizadi ine. Ndikuyamikani kaamba ka bukhu lozizwitsa mowonadi limeneli.”
Inunso mungakhale ndi bukhuli, limene limalingalira mafunso ali pamwambapa ndi ena ambiri, mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka. Kokha K8.00.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Your Youth—Getting the Best out of It. Ndatsekeramo K8.00 (Zambia).