Sawopanso Nkomwe
Kalata yolandiridwa posachedwapa ndi ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society mu German imaŵerenga, m’mbali ina kuti:
“Diana ali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa ndipo wakhala akuvutika ndi dzanzi la minofu kuyambira pamene anabadwa. Popeza iye amafunikira kupezeka pa sukulu yapadera makilomita ambiri kutali ndi kunyumba, iye amayenera kupita kukagona pa 7 koloko madzulo kotero kuti angakhale wokhoza kuwuka 6 koloko m’mawa wotsatira. Iye nthaŵi zonse ankachita mantha kukhala yekha m’chipinda chake. Chotero tinaikamo kaseti recorder ndi kuimbapo nyimbo pa kaseti, koma ichi sichinathandize. Pambali pa icho, ndinafuna kuti iye amvetsera ku chinachake chophunzitsa chomwe angathe kuchimvetsetsa.
“Kenaka yankho labwino kwambiri linabwera—makaseti onjambulidwa a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ndinawagula iwo kaamba ka iye, ndipo mwadzidzidzi Diana sanalinso ndi mantha nkomwe. Iye waphunzira khumi za nkhanizo pamtima—liwu ndi liwu—ndipo amadziŵa zinazo bwino lomwe kotero kuti angadziŵe chophophonya chimene ungapange ngati uŵerenga izo kwa iye, ngakhale kuti iyemwini panthaŵi ino sadziŵa kuŵerenga. Chiyambire pamene anaphunzira nkhani 69, ‘Mtsikana Athandiza Ngwazi,’ iye wakhala akulankhula kwa aphunzitsi ake ndi ana ku sukulu ponena za nkhani zimene amadziŵa.”
Kodi makaseti amenewa, limodzi ndi chofalitsidwa chokhala ndi zithunzi zokongola Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, zingakhale chiwonjezeko cholandiridwa ku laibrali ya mwana wanu? Ndi mwana wanji amene sangasangalatsidwe kukhala ndi wokamba nkhani woteroyo wokonzekera kuŵerenga kwa iye masana kapena usiku? Makaseti amenewa, limodzinso ndi bukhulo, angaordedwe mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kali pansipa.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, alubamu ya brown vinyl yokhala ndi makaseti anayi a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo (Chingelezi). Ndatsekeramo K54.00 (Zambia). [ ] Tumizani chofalitsidwa chokhala ndi zithunzithunzi cha masamba 256 Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K20.00 (Zambia). [ ] Chongani chimodzi kapena zonse ziŵiri, ndipo tumizani chopereka choyenera.