Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/1 tsamba 30
  • “Mawu Oyenera a pa Nthaŵi Yake”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mawu Oyenera a pa Nthaŵi Yake”
  • Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/1 tsamba 30

“Mawu Oyenera a pa Nthaŵi Yake”

“Mawu oyenera a pa nthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva,” imatero Miyambo 25:11. Mawu athu olingalirika ndi zochita zake zachifundo zingasonkhezere modekha mtima wa munthu wolungama ku njira za chivomerezo cha Yehova. Chinachake chimene tingakhale tinanena ngakhale kuchita, ngakhale zaka zambiri zapita, chingakumbukiridwebe mosangalala ndi munthu wina. Mwachitsanzo, pamene anali kuchezera mpingo, woyang’anira wadera ndi mkazi wake anali alendo a mlongo wobatizidwa cha posachedwa. Mkazi wa woyang’anira waderayo anatumiza kalata yothokoza m’kuyamikira kaamba ka kuchereza kumene kunasonyezedwa. Zaka zoposa zisanu ndi ziŵiri pambuyo pake, iye analandira kalata yotsatirayi:

“Ndadzimva kuti ndiyenera kokha kulemba ndi kukuuzani za thandizo limene inu mwakhala kwa ine mkati mwa zaka popanda kudziŵa kwanu chimenecho. Ndinali limodzi ndi inu ndi Jim kokha pa chakudya chochepa cha pamasana, ndipo munanditumizira kardi yabwino kwambiri ya chiyamikiro. Chinali chabwino koposa, koma linali lemba limene linafikira mtima wanga, ndipo sindinaliiwale ilo nkomwe. Umu munali mu 1976. Ndinali ndekha m’banja langa amene kwenikweni ndinali wosangalatsidwa ndi chowonadi. Ndinaphunzira ndi atsikana anga ndi kuyesera kukhala mkazi wabwino. Koma nthaŵi zina ndinafuna kukhala kunja, kunja kwa chowonadi, kunja kwa mathayo​—kokha kunja. Koma lemba limene munalemba linakoka mtima wanga, ndipo ndinakhoza kunena kwa ine mwini, ‘ndiri wadyera chotani,’ ndipo ndinapitirizabe.

“Palibe chinthu nchimodzi chomwe m’zaka zisanu ndi zitatu zimenezo chimene chinali ndi chiyambukiro chotero kwa ine, ndipo ndinafuna kukuuzani ponena za icho. Pambali pa lembalo, ndinalingalira kuti chinali chabwino chotani nanga kuti winawake wotanganitsidwa kwambiri monga mmene muliri mungatenge nthaŵi ya kundiyamikira ine kaamba ka kuchita chinachake chimene ndiyenera kumachichita.

“Aha, inde​—lembalo​—2 Yohane 8.

“Sandra”

Lerolino, mwamuna wa Sandra ali wobatizidwa ndipo amagwirizana naye monga wofalitsa wa mbiri yabwino. Mmodzi wa ana awo akazi aŵiri ali mpainiya wokhazikika, ndipo mwana wamkazi winayo wakhala akuchita upainiya wothandizira kuyambira pamene anamaliza maphunziro posachedwapa kuchokera ku sukulu yapamwamba.

Pomalizira, nchiyani chimene 2 Yohane 8 amanena? “Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena