Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 10/15 tsamba 32
  • Anaphonya Basi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anaphonya Basi
  • Nsanja ya Olonda—1987
Nsanja ya Olonda—1987
w87 10/15 tsamba 32

Anaphonya Basi

TSIKU lina James anawona mwana wake wamkazi Rebecca akuyenda mwachilendo mochedwa kupita kukakumana ndi basi ya ku sukulu. Ngakhale kuti Rebecca anawona basi ikubwera, iye anayenda ngakhale mochedwerapo ndipo mwadala anaphonya basiyo.

Madzulo amodzimodziwo James ndi mkazi wake, Veronica, anakambitsirana nkhaniyo mwakubwereramo m’nkhani ya “Yona ndi Chinsomba Chachikulu” kuchokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Inali imodzi ya nkhani za pamtima za Rebecca. Pambuyo pa kumaliza nkhaniyo, makolowo anaigwirizanitsa iyo ndi vuto la mwana wawo wamkazi. Iye anapeza nsonga yeniyeni ndi kunena kuti: “Ngakhale kuti Yona anathawa ndi kufika m’mavuto m’nyanja, ndipo iye anamezedwa ndi nsomba ndipo analavulidwa kunja​—ntchito yake kaamba ka Yehova inali kudikirabe kaamba ka iye kuichita.”

Tsiku lotsatira Rebecca anapita ku sukulu ndi kawonedwe katsopano ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo atalikupatira kukhwapa kwake.

Mungalandire kope la chofalitsidwa chochitiridwa chitsanzo mokongola, cha malemba a akulu, cha masamba 256 mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K20.00.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena