Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 9/1 tsamba 30-31
  • Chokwaniritsa Chozizwitsa cha Costa Rica

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chokwaniritsa Chozizwitsa cha Costa Rica
  • Nsanja ya Olonda—1987
Nsanja ya Olonda—1987
w87 9/1 tsamba 30-31

Chokwaniritsa Chozizwitsa cha Costa Rica

“MUKUCHITA zimene tangophunzira ponena za izo!” anachitira ndemanga chotero injiniya wa zomangamanga yemwe anabwera kudzawona nthambi yatsopano ikumangidwa mamailosi asanu ndi aŵiri (11 km) kunja kwa San José, Costa Rica.

Kodi nchiyani chimene chinali chozizwitsa ponena za nyumba zimenezi? Iwo anali kumanga ndi njira ya kutukula​—yoyambirira mu Costa Rica. Maziko ndi nsanamira zinamangidwa choyamba. Kenaka, pa malo pomwepo, mbali za simenti za makoma zinaikidwa chimodzi pamwamba pa chinzake mowunjikidwa. Zigawo za khoma zopangidwiratu zimenezi kenaka zinatukulidwa ndi kunyamulidwa ndi makina onyamulira zinthu ndipo zinawotchereredwa m’malo awo oyenerera. Pomalizira, denga linaikidwa, ndipo zonse zomwe zinatsala kuti zichitidwe zinali kumaliza kotsirizira.

Projeketi imeneyi inalinso kuyesera koyambirira kwa Watch Tower Society kwa kumanga nyumba mwa njira ya kutukula, kunja kwa United States. Kaamba ka chifukwa ichi, ogwira ntchito ochokera ku nthambi zina omwe akukonzekera kumanga kapena kufutukuka anali pamalopo kuwona mmene njirayo inagwirira ntchito. Amene analiponso, anali mainjiniya ndi okonza mapulani a nyumba ochokera kumbali zina. Onse anali osangalatsidwa ndi zimene anawona.

Nyumbazo zinamangidwa mu mtundu wokongola wachikale wa chiSpanish, ndi denga la malata ofiira ndi mazenera opindikira kunja. Msewu wopita mozungulira munda wozungulira umatsogolera ku chipata chachikulu ndi malo olandirira alendo. Cha kumanja kuli nyumba zosanjikizana ziŵiri, nyumba yokhalamo anthu ya zipinda 24 yokhala ndi chipinda chachikulu cha banja chomwe chiri ndi laibulale, malo ophunzirira, ndi malo a moto okongola. Cholumikizidwa ku ichi chiri chipinda chodyeramo cha mipando 100, ndi kichini ya makono ndi chipinda chochapiramo zovala. Kumbali ina ya bwalolo kuli nyumba ya ofesi yokhala ndi maofesi 13 imodzi ndi imodzi ndi chipinda cha msonkhano chokhazikitsidwa mozungulira bwalo lapoyera la munda wa maluŵa a ku malo otentha pansi pa thambo lowunikiridwa. Nyumba yaikulu cha kumanzere iri nyumba yosungiramo zinthu kaamba ka kusungiramo mabukhu ndi zinthu zina.

Aliyense amene anabwera kudzachezera anazizwa ndi zimene anawona. Zomvedwa mobwerezabwereza zinali ndemanga zonga ngati izi: “Ndi ntchito yabwino chotani nanga!” “Sindinawonepo ndi kale lonse china chake chokongola monga ichi!” “Iyi mwachiwonekere iri ntchito yachikondi.”

Ndithudi, zonsezi zinathekera chifukwa cha “ntchito yachikondi.” Abale ndi alongo oposa 4,700, kuphatikizapo 295 ochokera ku maiko ena, anagwira ntchito kwa miyezi 24 pa projekitiyo. Zambiri za zipangizo ndi zinthu zinapangidwa pamalopo. Mwachitsanzo, pa chiyambi penipeni chotukulira zinthu pa nyumba zosanjikizidwa ziŵiri, mwachikondi chodziŵika kwa abalewo monga Julio, chinamangidwa. Zosakanizira simenti zotchedwa Bertha ndi Martha zinagulidwa ndi kufufuzidwa ndi kuyesedwa kaamba ka projekitiyo. Nyali, mawaya a magetsi, ntchito ya zitsulo zotenthedwa kuti zilimbe, masitepi ndi malo a pansi pa masitepi a miyala yonyezimira ya Palladian, ndi zina zotero, zonsezo zinapangidwa ndi abale omwe analibe chidziŵitso chachindunji mu madera amenewa. “Kutenthedwa mtima kaamba ka projekitiyo kumbali ya abale kuchokera mu dziko limeneli kunali kozizwitsa,” analengeza motero woyang’anira wa projekitiyo.

Utali wa kutenthedwa maganizo unasonyezedwa pa January 4, 1987, pamene khamu la anthu 13,111 linabwera kaamba ka kupereka. Khonde lambali ya kumadzulo kwa chipinda cha banja linagwiritsiridwa ntchito monga pulatiformu ndipo khamu linasonkhana pa bwalo lalikulu pansi. Abale M. G. Henschel ndi L. A. Swingle a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anali alankhuli enieni pa programu. Nkhani yotenthetsa mtima ya Mbale Swingle inali pa mutu wakuti “Yehova Akupitiriza Kuchipanga Icho Kukula,” ndipo m’nkhani ya kupereka, Mbale Henschel anathandiza onse kuyamikira kuti nyumba yokongola imeneyo iri yathandizo kwa anthu a Yehova kokha ngati iwo apitiriza kutulutsa zipatso za mzimu wake.

Zosonkhanitsidwa pamodzi kaamba ka chochitika chapadera chimenechi zinali ziwalo za banja la amishonale loyambirira la Gileadi mu Costa Rica. Tsopano achikulire, iwo mozama anafulumizidwa ndi kuyanjanitsidwanso kumeneku ndi chitsimikiziro chowoneka cha dalitso lolemera la Yehova pa ntchito yolalikira Ufumu mu Costa Rica mkati mwa zaka. Limodzi ndi kuperekedwa kozizwitsa kumeneku kwa nyumba yaikulu yoteroyo, yopumitsa bwino, ndi yoyenerera, awo onse amene analipo anali ndi chidaliro kuti dzina la Yehova lidzakulitsidwa mowonjezereka mu dziko ili la ku malo otentha.

[Zithunzi patsamba 31]

Mbali ya khoma yoikidwiratu ikutukulidwa . . . ndi kuikidwa m’malo

Msewu wozungulira umatsogoza ku nyumba yomangidwa m’mtundu wachikale wa chiSpanish

Mbali ya khamu lotenthedwa maganizo pa tsiku la kupereka

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena