Ripoti la Olengeza Ufumu
Chowonadi cha Baibulo Chimamasula Kuchoka ku Kukhulupirira Mizimu
KAWONEDWE ka Yehova ka kukhulupirira mizimu kanalongosoledwa bwino kwa Aisrayeli mu mawu awa: “Musamachita nyanga, kapena kuwombeza ula.” (Levitiko 19:26) Koma kodi ndimotani mmene wina amene ali wolowetsedwa mu matsenga ndi kukhulupirira mizimu angawomboledwere kuchokera ku mphamvu ya ziwanda? Yesu anati: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Ichi chinatsimikiziridwa kukhala chowona, monga chawonedwa mu chokumana nacho chotsatirachi cha Mboni mu France.
“Pamene ndinasamukira kunyumba yanga yatsopano, ndinali nditangokhazikika kumene pamene mnansi waubwenzi anabwera kuzungulira ndipo anadzipereka kusonyeza za mtsogolo mwanga. Mwamsanga ndinalingalira kusakhala ndi china chake chowonjezeka kuchita naye, chomwe sichinali chinthu chochepa, popeza kuti iye kwenikweni analidi wamakhalidwe amayanjano koposa.
“Mu November 1980 ndinadwala, ndipo anabwera kudzapereka thandizo. Ndinafikira ku kuyamikira kukoma mtima kwake. Ndinakokeredwa kwa iye mwathithithi pamene iye ananena kuti kaŵirikaŵiri angadzutse kutsamwidwa kuchokera ku chisoni. Kenaka ndinazindikira kuti iye sanali wachimwemwe monga mmene ndinalingalirira. Koma kodi ndimotani mmene vuto limeneli la kukhulupirira mizimu likathetsedwera? Ndikumadzimva kuti sindikanatha kudikira ndi pang’ono pomwe, ndinagamulapo kulankhula ndi iye ponena za chowonadi.
“Tinayamba kukambitsirana za mavuto a ndalama ofala kwa ife akazi osakwatiwa. Iye kenaka anati: ‘Ndiri ndi yankho. Ndimapanga makadi odziŵa kuŵerenga ndalama.’ Chotero ndinatulutsa Baibulo langa ndi kumusonyeza iye mmene chinaliri chowopsya kugwirizana ndi magwero oipa a mphamvu kwambiri.
“Ichi chinayambitsa kukambitsirana kosamalitsa pa kukhulupirira mizimu. Iye analongosola kuti chirichonse chimene ananeneratu chinakhala chowona. Ndinayesa kumthandiza iye kulingalira zinthuzo. Ndinapitiriza kumusonyeza iye mawu a Mose a pa Deuteronomo 18:10, 11: Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga . . . kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Pamene ndinali kuchoka, iye ananena: ‘Kungolingalira kokha kuti ndinakhulupirira kuti ndinapeza yankho kumavuto anga.’ Mawu amenewa anandilimbikitsa chotani nanga, popeza iye pano, pambuyo pa kukambitsirana kumodzi kokha, anali kulankhula ponena za mizimu m’mkhalidwe wa kale! Kwa ine icho chinatanthauza kuti mkati mwake anali atagwira nsonga yeniyeni.
“Wokhala ndi kukokeredwa kokhoza kukhutiritsidwa ku chakudya chauzimu, iye anali kuŵerenga Baibulo kufikira ora lachitatu kapena lachinayi m’mawa. Kuti tiyambe, tinali ndi maphunziro aŵiri pa mlungu mmodzi. Iye anapezeka pa msonkhano ndi kupanga kupita patsogolo kofulumira. Komabe, ife motheratu tinalowa mu phunziro la kukhulupirira mizimu, kugwiritsira ntchito Baibulo ndi zofalitsidwa za Watch Tower, ndipo iye anapanga chosankha chaumwini kutentha chirichonse chimene anali nacho chogwirizana ndi ziwanda.
“Mkaziyu anapirira ndipo mwamsanga anali kunja kulalikira ‘mbiri yabwino’ kwa ena. Kwa nthaŵi ndi nthaŵi iye analandira lamya kuchokera kwa omwe anali akasitomala ake, ndipo pambuyo pa kulongosola kuti iye anali ataleka machitachita ake akukhulupirira mizimu, iye anawaitana iwo kukamva ponena za china chake chosangalatsa koposa. Iye anabatizidwa ndipo tsopano ali mlongo wathu.”