Lipoti la Olengeza Ufumu
Chile Apita Patsogolo ndi Kuwunikira Kowonjezereka
MONGA dzuwa lowala kwambiri lomawala pamwamba pa mapiri a Andes mbandakucha, kuwala kwa chowonadi cha Baibulo poyamba kunafika ku Chile mu 1930. Mu chaka chimenecho, mmodzi wa atumiki odzipereka a Yehova anabwera kuchokera ku Argentina ndi mbiri yabwino. Lerolino, kuwala kwa Mawu a Mulungu kwaunikira ndipo kwafikira kungodya zakutali za dzikolo.
Pamene ofesi ya nthambi yoyamba ya mu Chile inakhazikitsidwa mu 1945, nyumba ya nthambi yaikulu, yatsopano, inamangidwa mu 1970, pamene chiwerengero cha olengeza Ufumu chinafika 7, 000. Mu zaka khumi zotsatira, kuwunikira kowonjezereka kuchokera mu Mawu a Mulungu kunakhudza mitima yabwino yambiri. Pofika kumayambiriro kwa mu ma-1980 kufutukulika kowonjezereka kwa ofesi ya nthambi kunafunidwa mwamsanga. Chotero, mu September 1982 malo a 17. 5 acre (7 ha) kunja kwa mzinda wa Santiago anagulidwa. Ndipo pambuyo pa ntchito yochuluka yoyambirira, kukumba kunayambidwa mu June 1984.
Chinali chotenthetsa mtima kuwona ndimotani mmene abale a ku Chile achichepere ndi achikulire, anachirikizira ntchitoyo ndi zopereka zawo zoolowa manja. Zikwi za ena zinapereka nthawi yawo ndi maluso awo. Ena okhala ndi maphunziro odziwa zopangapanga anathandiza ndi kukonza makina owonongeka. Ena anagwira ntchito ya matabwa, kuwotcherera zitsulo, kupanga zochinga, ndi kukongoletsa panja, kapena kupereka ntchito yachikondi mwakuchotsa zinyalala, kukankha mawilubala, ndi kukumba mayenje. Indedi, kuwala kopita patsogolo kwa Mawu a Mulungu kwakhudza mitima ya anthu ake ndi kuwafulumiza iwo kudzipereka iwo eni.—Masalmo 110:3.
Umodzi ndi kudzipereka kwa iwo eni sikunapulumuke kuzindikiridwa ndi akunja. Anthu ogulitsa ambiri ndipo ngakhale ophunzira pa yuniversite ndi maprofesala anabwera kumalo omangawo kudzawona ndi kuphunzira. Womanga mmodzi anafuna kulemba ntchito gulu lonse lomwe linali kumanga chipupa, kuti likamthandiza iye ndi nyumba yogulitsiramo yomwe anali kumanga. Wogulitsa anachitira ndemanga kuti ndi mosiyana chotani nanga mmene gulu logwira ntchitolo linaliri—osalumbira, osanyalanyaza ntchito. Pamene anali kuuzidwa kuti onse anali Mboni za Yehova ndipo anali pamenepo monga odzipereka, iye anayankha: “Wina sangawone ichi kumbali ina iriyonse. Anthu inu muli a dziko lina lake.”
Pomalizira, mu August 1986 ziwalo za nthambi ya Chile zinasamukira kumalo atsopano mu Puente Alto. Ndipo pa October 25, ndi kupezekapo kwa A. D. Schroeder wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, khamu lanthumanzi la anthu 933 linafuula chirikizo lawo lochokera mu mtima mu kupereka nyumba yatsopano imeneyi ku utumiki wa Yehova. Tsiku lotsatira, chochitika chapadera chinachitidwa pa bwalo la mpira lapafupipo, ndipo 18, 012 anawonjezera si yawo ku chimangocho.
Kodi kufutukuka kumeneko kulidi koyenerera? Lolani nsonga zipereke yankho. Pamene malowo anagulidwa mu 1982, kunali ofalitsa a ufumu 17, 500 mu Chile. Tsopano analipo oposa 29, 000! Ndipo ndi chifupifupi maphunziro a Baibulo apanyumba 40, 000 akutsogozedwa, palibe mapeto amene akuwonekera. Chotero lolani kuwala kochokera ku Mawu a Mulungu kuwale mopitirira mowalitsa mu gawo ili la chonde pa mapazi a phiri la Andes, ku chilemekezo cha Yehova ndi dalitso la anthu ake.—Danieli 12:3.