Kusangalala Limodzi ndi Kalasi ya Gileadi ya 82
“IFE SITIRI Akristu amunyengo yabwino. Ife tiri kokha achimwemwe kukhala pano.” Ndi mawu amenewo tcheyamani anatsegulira tsiku lapadera la nthawi zonse la msonkhano pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova mu Jersey City pa Sande, tsiku loyamba la March. Kunja, kunali mvula yamphamvu. Mkati, linali tsiku la kumaliza maphunziro kaamba ka ophunzira 24 a kalasi ya Gileadi ya 82. Akuyang’ana pa nkhope zachimwemwe za ophunzira wo, tcheyamani Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira anapitiriza kunena kuti: “Chiri chodziwikiratu kuti iwo ali ofunitsitsa ndi achimwemwe ponena za ziyembekezo zawo. Popeza Baibulo limati ‘sangalala ndi anthu amene akusangalala,’ ndiri wotsimikiza kuti tonse a ife tikudzimva m’njira yofananayo!” Kuwomba mmanja komwe kunalandira ndemanga imeneyi kunatsimikizira kuti opezekapo onse 4, 557 anavomereza.
Mlankhuli woyamba pa programuyo anali John Barr, yemwenso ali chiwalo cha Bungwe Lolamulira. Akumagwira mawu mochulukira kuchokera ku Masalmo 104, iye anasonyeza kuti Yehova sanalenge kokha chirichonse, zamoyo ndi zopanda moyo, komanso analenga malo kaamba ka cholengedwa chirichonse kukhalapo. Iye anapitiriza kunena kuti: “Tsopano, pamene mupita ku gawo lanu, lingalirani: ‘Yehova wandikhazikitsa ine pano.’ Musadzaiwale nkomwe ichi.”
Wotsatira kulankhula anali chiwalo cha Komiti ya Watchtower Farms, John Stuefloten. Iye anakumbutsa ophunzirawo kuti: “Mwambo umatiuza ife kuti: ‘ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake.’ ” (Miyambo 9:9) Kwa miyezi isanu ophunzirawo akhala akupatsidwa chakudya chauzimu cholemera. Mosakaikira, pa tsiku lakumaliza maphunziroli iwo anadzimva odzaza mwauzimu. “Koma,” anatero mlankhuliyo, “inu mwangoyamba kumene!” Iye analimbikitsa ophunzirawo kupitirizabe kukula mu nzeru ndi chifundo kotero kuti akhale okhoza kuthandiza ena—Miyambo 3:27.
George Gangas wa Bungwe Lolamulira anatsatira ndi mawu osankhidwa bwino ponena za chimwemwe. Iye anakumbutsa omaliza maphunzirowo kuti iwo akutumikira “Mulungu wachimwemwe” ndipo analegeza kuti: “Mudzapeza chimwemwe mu gawo lanu lachilendo.” Chifukwa ninji? “Chifukwa Yehova akukutumizani inu kukawombola anthu mu ukapolo.”
George Couch wa mu Komiti ya Brooklyn Beteli analankhula ponena za kudera nkhaŵa. Iye anazindikira kuti ophunzirawo sanali achilendo ku kudera nkhaWa. Chitokoso cha kubwera ku Gileadi, kukhala mu Beteli ya ku Brooklyn, ndi kulalikira mu mzinda wa New York zonse zinapangitsa kudera nkhaŵa kwina kwake. Tsopano ophunzirawo anali odera nkhaŵa ponena za ntchito yawo ya umishonale. Koma kudera nkhawa koyenerera sikuli mdani. “Kudera nkhawa kungatithandize kuchita kuthekera kwathu kwabwino,” iye analongosola tero, ndipo iye analimbikitsa ophunzirawo kukhulupirira Yehova ndi kuchita kuthekera kwawo mu magawo awo.
Mlangizi wa Sukuluyo Jack Redford kenaka anatsatira pa bwalolo. Iye anachenjeza ponena za kusuliza kosalungamitsidwa. Akumagwira mawu zitsanzo za mu Baibulo za kuweruza mwamsanga komwe pambuyo pake kunayambitsa mavuto, iye anagwira mawu a Yesu akuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. ” (Mateyu 7:1) Kalasi la 82 linayimira Mulungu wachikondi. Ophunzirawo anali kutumizidwa ku magawo awo kukamvera chisoni, osati kusuliza.
Mlangizi wa Gileadi Ulysses Glass anagwira mawu mwambo wa Baibulo: “Omwe athamanga msanga sapambana liwiro, ngakhale olimba sapambana mu nkhondo.” (Mlaliki 9:11) Chotulukapo cha nkhani kaŵirikaŵiri sichimadalira pa kuthekera kwathu kwa chibadwa. Mu ntchito ya umishonale, chimakhala kawirikawiri nkhani ya chikhulupiriro ndi kufunitsitsa kulandira chitokoso. Mlankhuliyo anayamikira kalasi ya 82 kaamba ka kukhala yokhazikika, yodalirika, ndi yogwirizanika. Mikhalidwe yoteroyo ikawapangitsa iwo kukhala pa malo okhazikika bwino.
Mlankhuli womalizira wa mmawa, prezidenti wa Watch Tower Society Frederick Franz, analengeza kuti kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 82 kunatsimikizira chikhulupiriro cha awo amene anayambitsa sukuluyo kubwerera m’mbuyo mmasiku owopsya a Nkhondo ya Dziko II. Iye analankhula pa dzina lakuti Gileadi, akumati liri liwu la Baibulo lotanthauz’a “Mulu wa Mboni” (Yerekezani ndi Genesis 31:43-53. ) Amishonale a Gileadi amene amakhalabe okhulupirika mu mathayo awo amatumikira monga mulu wa mboni Iwo ali chitsimikizo chamoyo cha chowonadi.
Ophunzirawo kenako analandira zikalata zawo zakumaliza maphunziro, ndipo mmawa munatha ndi kuwerenga kalata ya chithokozo kuchokera ku kalasi la 82. Ophunzirawo anazindirika kuti ‘madalitso a Yehova alemeretsa.’ Mchiyang’aniro cha chimenecho, iwo anati, “Yehova watipangitsa ife kudzimva monga anthu 24 olemera kwambiri pa dziko lonse lapansi!”—Miyambo 10:22.
Masana, pambuyo pa phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda, ophunzirawo anasonyeza programu yosangalatsa. Iyo inatha ndi mawu achiyamikiro ochokera mu mtima kwa makolo awo, amene kaamba ka kusadzikonda kwawo ndi chirikizo lawo analola ana awo kuchoka ndi kukhala amishonale.
Programu ya ophunzirawo inatsatiridwa ndi kuperekedwa kwa chitsanzo cha pa nthaŵi yake, pambuyo pa chimene tcheyamani Theodore Jaracz, anapereka ndemanga zina zomalizira. Ndipo ndi chozizwitsa chotani nanga. chimene Sosaite inali nacho kaamba ka mphindi zotsekera zimenezo! Mlankhuliyo analengeza kuti posachedwapa Sosaite idzatsegula sukulu yatsopano, Sukulu ya Maphunziro a Utumiki, yophunzitsa poyamba akulu ndi atumiki otumikira osakwatira. Onse anatenga chidziwitso chapadera pamene tcheyamani analengeza chimodzi cha ziyeneretso za kupezeka pa sukulu yatsopanoyo: Kufunitsitsa “kutumikira kulikonse kumene kuli kusowa mmunda wa dziko lonse.”
Kuwomba m’manja kotenthedwa maganizo kunalandira mbiri imeneyo ponena za sukulu yatsopano imeneyo. (Tsatanetsatane wowonjezereka wa ichi waperekedwa mu nkhani yotsatira. ) Programuyo kenaka inamaliza ndi nyimbo ndi pemphero la chiyamikiro kwa Yehova. Aliyense kenaka anatuluka kunja madzulo a mitambo mu New Jersey. Kunali kudakali mvula yochepera, koma ochepera anadera nkhawa ponena za iyo. Mitima yonse inali idakali ndi chisangalalo cha kumaliza maphunziro kwa kalasi ya Gileadi ya 82.
[Chithunzi patsamba 26
Omaliza Maphunziro a Kalasi ya 82 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
Mndandanda pansipa, mizera yawerengedwa kuyambira kutsogolo kunka kumbuyo, ndipo maina anandandalitsidwa kuchokera ku lamanzere kunka ku lamanja mu mzera uliwonse.
(1) Gish, L. ; Evans, E. ; Dean, S. ; Hanson, R. ; Suomalainen, A. ; DuBose, D.
(2) Wallenberg, P. ; Wallenberg, M. ; Bauer, O. ; Suomalainen, H. ; Taylor, B. ; DiStefano, G.
(3) Scott, K. ; Evans, M. ; Taylor, A. , Jr. ; Lindby, J. ; Hanson, C. ; Holmkvist, M.
(4) Sampson, T. ; Gish, T. ; Ball, D. ; DuBose, J. ; Dean, T. ; Scott, D.