Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/1 tsamba 21
  • Mphoto ya Kukhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphoto ya Kukhulupirika
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Mawu a Mulungu Anakula”
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Otsimikiza Mtima Kutumikira Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/1 tsamba 21

Lipoti la Olengeza Ufumu

Mphoto ya Kukhulupirika

MUNALI MU Italy kuti, zaka 15 zapita, Mrs. B​—, panthawiyo a zaka 15, anadziwa chowonadi. Komabe, iwo sanapite patsogolo, ndipo chotero anakwatiwa ndi wosakhulupirira. Mbewu za chowonadi zinatsalira mu mtima mwawo, ngakhale kuli tero, ndipo chifupifupi chaka chimodzi chapita iwo anavomereza phunziro la Baibulo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kuyamba kupezeka pa misonkhano. Mwamuna wawo mwachiwawa anatsutsa ndi kuwopsyeza kuwapanga iwo kuchoka panyumba. lye anawamenya iwo moipitsitsa kotero kuti anafunikira chisamaliro cha adokotala. Pa usiku umodzi iye analowa mu Nyumba ya Ufumu mkati mwa msonkhano, kumenya mbale, kuphwanya galasi la pa chitseko, ndi kupfuula mwaukali.

Pamene iwo anabwerera kunyumba, anapeza kuti mwamuna wawo wawatsekera kunja. Mosataya kulimba mtima kwawo, iwo anapita ku ofesi ya carabinieri (apolisi) kuwadziwitsa iwo za chimene chinali kuchitika ndipo kenaka anapita kukagona kunyumba ya azakhali awo. Pambuyo pa masiku awiri mwamuna wawo anawalola iwo kubwerera kunyumba.

Mwamunayo ali wotchuka kwambiri mu mzinda. lye anayamba kunyoza Mboni za Yehova mwapoyera, akumanena kuti izo zasokoneza banja lake. Mu ndawala imeneyo yotsutsa Mboni, iye anachirikizidwa ndi atsogoleri achipembedzo. Wansembe anali ndi timapepala tokhoza kumatika tokhala ndi mawu otsatirawa: “MBONI ZA YEHOVA: Musasokoneze mtendere wa banja iri. ZIKOMOI” lye anapangitsa timapepala tomamatiza timeneti kuikidwa pa zitseko mu mzindawo. Aliyense anali kulankhula ponena za Mboni za Yehova ndi kuzipanga izo maziko akuseka kwawo ndi kunyodola. Mosasamala kanthu za chimenechi, abale anatenga kulimba mtima ndi kupitirizabe kupita patsogolo mu utumiki wawo mwachangu kuposa ndi kale lonse. Mabanja ambiri sanafune mapepala omamatiza amenewo pa zitseko zawo. Anyamata ena, anatumizidwa ndi ansembe, anapatsidwa 100 lire kaamba ka kumatika mapepalawo pa zitseko, chinachitiridwa ripoti.

Panthawiyo Mr. B​—​anadziwitsa mkazi wawo kuti anayenera kuchoka ku nyumba, popeza iye anali kutenga masitepi oyenerera kaamba ka kupatukana kwalamulo. Koma zinthu zinali kuyamba kusintha mu mzindawo. Nyumba ya wailesi ya kumaloko inapereka programu, ndipo wosimbayo analongosola nkhaniyo monga “kachitidwe ka kulawa kokaikiritsa, kwa khalidwe loipa.” Mkati mwa programuyo, abale athu analongosola kuti mabanja ambiri anali ndi timapepala tomamatizidwato tokakamizidwa pa iwo. Ichi chinatsimikiziridwa ndi chenicheni chakuti ito tinaikidwa mkati mwa usiku ngakhale pa zitseko za zina za Mboniza Yehova ndi mabanja ena omwe anali kulandira kuchezera kwawo. Wochita ripoti wa pa wailesiyo analemekeza Mboni za Yehova ndi kunena kuti iwo anali anthu “okhala ndi ulemu wapadera, ndi kuti anali ndi chifundo chapamwamba koposa.”

Pomalizira, nthawi inafika kaamba ka awiriwo kuwonekera pamaso pa woweruza kuyamba mlandu wawo wa kulekana mwalamulo womwe mwamunayo anali atafunsira. Woweruzayo analemekeza Mrs B​—​kaamba ka chikhumbo chawo cha kusafuna kulekana, ndipo pamene iwo anali kudikira kaamba kalamulo, iye anawapatsa iwo mwawi wa kusunga ana. Iwo adzapitiriza kukhala mu nyumba yawo, ndipo mwamuna wawo anayenera kuwapatsa iwo 250, 000 lire pa mwezi. Mwamunayo anakana, akumanena kuti: “Nyumbayo iri katundu wa mayi wanga, ndipo mkazi wanga sangakhale mmenemo.” Woweruza anayankha: “Iwe ukufuna kukhala mwamuna ndi wolamula. Mkazi wako nthawi zonse ayenera kunena inde ndipo kwanthawi yoyamba iye wanena ayi. Chotero iwe ukupangitsa mzinda wonse kukhala muphokoso. Ngati mkazi wako anakhala wosakhulupirika kwa iwe, ine ndikanamvetsetsa chimenecho. Koma chenicheni chakuti iye akutsatira chikhulupiriro chimodzi m’malo mwa china sichiri chirichonse chimene chiyenera kuchita ndi iwe.”

Mrs. B​—​tsopano akutumikira Yehova mwachimwemwe. (Mateyu 5:10) Anthu a mu mzindawo asintha kawonedwe kawo, ndipo kukambitsirana kwa Baibulo kozizwitsa kukuchitika. Iwo akuvomereza kuti siziri Mboni za Yehova zomwe zimasokoneza mtendere wa banja. Ngati padakali mapepala omamatiza pa zitseko, iwo alibe tanthauzo ndi komwe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena