Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 32
  • Kumachita Nawo Malingaliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumachita Nawo Malingaliro
  • Nsanja ya Olonda—1987
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 32

Kumachita Nawo Malingaliro

Kuchita nawo malingaliro athu mwachipambano chiri chitokoso chenicheni. Wachichepere akunena za chokumana nacho chake: “Ndinali kudzimva wachimwemwe, koma mphindi yotsatira ndinali watondovi. Nthawi zina sindinali kudziwa chimene malingaliro anga anali. Chinali ngati kuti ndinali wotaika kotheratu mu mdima. Sindikanatha kudzilongosola ine mwini ndi chimene malingaliro anga anali mosasamala kathu kuti ndi kwayani komwe ndinalankhula, wosati angakhale kwa ine mwini. Ndinadzimva kukhala ngati sindinali kupeza chisamaliro kuchokera kwa anthu ondizungulira, makamaka anzanga a ku sukulu, chifukwa sindinali wokongola kwenikweni. Potsirizira malingaliro onsewa anali kundipha mkati, ndipo ndinayamba kudzida ine mwini ndi umunthu wanga.”

Mtsikanayo anapeza kope la bukhu la Your Youth​—Getting the Best out of It. “Ilo linali losangalatsa kwambiri,“ iye akulemba, “chotero ndinafuna kuwerenga mutu wakuti ’Kufika Kuukazi.’ Sindinathe kukhulupirira zomwe ndinali kuwerenga chifukwa chakuti mutu umenewu unalongosola kwenikweni momwe ndinali kumverera chaposachedwa, ndipo linapereka yankho. Chinali cholimbikitsa kuwerenga kuti sichinali chachilendo kumva motero. Ndinayenera kokha kudziwa njira yolondola ya kusamalira izo.”

Pambali pa kuthandiza achichepere kuchita ndi malingaliro awo, bukhuli limalingalira nkhani monga ngati za phyotophyoto, ndipo limayankha mafunso akuti, Kodi achichepere ayenera kumwa zakumwa zoledzeretsa ndipo, Kodi ayenera kugonana asanakwatirane? Landirani kope pa K5. 00 yokha mwakudzaza ndi kutumiza katikiti kotsatiraka.

Chonde tumizani, mutalipiliratu positi, bukhu la chikuto cholimba, (mu Chingelezi) lamasamba 192 la Your Youth​—Getting the Best out of It. Ndatumiza K5. 00.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena