Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 8/8 tsamba 32
  • Chofalitsa Chokhala ndi Cholinga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chofalitsa Chokhala ndi Cholinga
  • Galamukani!—1999
Galamukani!—1999
g99 8/8 tsamba 32

Chofalitsa Chokhala ndi Cholinga

MKULU woyang’anira laibulale ina yaboma ku Prague, m’dziko la Czech Republic, anamata pabolodi lachidziŵitso m’laibulaleyo nkhani ya masamba aŵiri yolongosola za Galamukani! Zina mwa zinthu zimene analemba ndi izi:

“Ine si wa Mboni za Yehova. Sikutinso ndimagwirizana nawo kwambiri kapena kudana kwambiri ndi Watch Tower Society. Komabe, sindingachitire mwina koma kuyamikira kuchokera pansi pamtima magazini a Galamukani!, amene ndakhala ndikuŵerenga kwa kanthaŵi ndithu. Ngakhale kungoŵerenga chabe mutu wake kamodzi patsiku kungakuthandizeni kwambiri. Ali ndi nkhani zabwino kwambiri zowonjezera pa nkhani za m’magazini amalonda; komabe, osati kungoŵerenga mutu wapachikuto wokhawo komanso nkhani zam’kati mwa magaziniyo . . .

“Galamukani! imakhala ndi nkhani zofufuzidwa bwino. Imalemba nkhani zimene magazini ena, pazifukwa zosiyanasiyana, safuna kuzitchula n’komwe. Imanena za zochitika ndi zotsatirapo zake, imaphunzitsa anthu kuzindikira zimene zikuchitika padziko lonse . . . Galamukani! siimaweruza. Imanena zoona ndiponso imasimba nkhani mmene oidziŵa bwino amaionera. Imasonyeza mbali zonse za ubwino kapena kuipa kwa chinachake, imasonyeza malemba ochokera m’Baibulo polongosola mavuto amene alipo lerowa, ndipo imasiyira pomwepo kuti woŵerengayo aone yekha chimene chili chabwino. Ndiponsotu Galamukani! imafunsa ndipo imaphunzitsa aŵerengi ake kufunsa—mafunso.”

Magazini iliyonse imalongosola patsamba 4 pambali yakuti “Chifukwa chake Galamukani! amafalitsidwa” kuti: “Chofunika koposa, magazini ano amalimbikitsa chidaliro mu lonjezo la Mlengi la dziko latsopano lamtendere ndi losungika limene lili pafupi kuloŵa m’malo dongosolo la zinthu lilipoli, loipa ndi losayeruzika.”

Lonjezo limeneli mungalipeze m’magawo aŵiri otsiriza a Bolosha la masamba 32 lotchedwa Kodi Chifuno cha Moyo n’Chiyani? Kodi Mungachipeze Motani? Zigawo zimenezi zili ndi mitu yakuti “Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa” ndi “Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso” Mungathe kulandira Boloshali polemba zofunika m’kabokosi kali pamusika ndi kukatumiza ku adiresi yasonyezedwapoyo kapena ku adiresi iliyonse imene ili yoyenera imene yasonyezedwa patsamba 5 la magazini ino.

□ Munditumizire bolosha yakuti Kodi Chifuno cha Moyo n’Chiyani? Kodi Mungachipeze Motani?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulele.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena