Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 2/8 tsamba 3
  • Kodi Mulungu Alikodi? Asayansi Ena Akuyankha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Alikodi? Asayansi Ena Akuyankha
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • Thambo Lathu Lodabwitsali—Kodi Linangokhalako Mwamwayi?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 2/8 tsamba 3

Kodi Mulungu Alikodi? Asayansi Ena Akuyankha

POLOFESA wa sayansi ya physics Ulrich J. Becker, wa pa sukulu ya zasayansi, ya Massachusetts Institute of Technology, atafunsidwa za Mulungu, anayankha kuti: “Kodi ineyo ndikanakhalako bwanji popanda wondilenga? Sindikudziŵa ngati palinso yankho lina lomveka kuposa pamenepo.”

Kodi mawu akewo anasemphana ndi maganizo ake pa zasayansi? Polofesayo kuyankha kwake kogometsa anati: “Ngati unaona mmene gudumu la ‘koloko’ limazungulirira—ungadziŵenso mmene magudumu enawo akuzungulirira, koma usaganize kuti ukatero ndiye kuti wadziŵa sayansi, ndipo usavutike ndi kuyankha funso lakuti anakunga sipiring’i ndani.”

Ena amangoona kuganiza molakwika, koma anthu ambiri olemekezeka a zasayansi sakaniratu mfundo yoti Mulungu aliko—Wanzeru Wamkulu yemwe analenga miyamba limodzi ndi munthu.

Taganizirani zitsanzo zina ziŵiri pamfundoyi. Polofesa wina wamasamu, John E. Fornaess, wa pa Yunivesite ya Princeton, pamene anafunsidwa maganizo ake ngati kunja kuno Mulungu aliko, anayankha kuti: “Ndimakhulupirira kuti Mulungu alikodi ndi kutinso Mulungu ndiye anapanga zonse zakuthambo, chilichonse kungoyambira zinthu zazing’ono mpaka zinthu zamoyo ndiponso magulu a milalang’amba ya nyenyezi.”

Polofesa winanso wa sayansi ya physics Henry Margenau, wa pa Yunivesite ya Yale, anati amakhulupirira kuti Mulungu ndiye analenga malamulo a chilengedwe, anawonjezeranso kuti: “Mulungu analenga zonse zakuthambo mosagwiritsa ntchito chilichonse, anazilenga mwa njira imenenso inayambitsa kuti pakhale chinthu chotchedwa nthaŵi.” Ndiyeno anadzatchula mfundo ina ili m’buku lakuti Mystery of Life’s Origin, kuti mmenemomo, asayansi ena atatu anafotokoza kuti kulongosola komveka n’kwakuti moyo anauyambitsa anali Mlengi. Wina wofufuza za mumlengalenga, Fred Hoyle, anali ndi maganizo ofanana; anati, kukhulupirira kuti selo loyamba kukhalapo linayambika mwamwayi, kuli ngati kukhulupirira kuti, zitsulo za ndege yamtundu wa Boeing 747 zoikidwa pabwalo, chilichonse pachokha, ndiyeno patabwera namondwe n’kuziulutsa zitsulo zonsezo, zingamangirirane n’kukhala ndege yamtundu wa 747.

Pa mayankho onsewa tingawonjezereponso mawu a Paulo yemwe analemba Baibulo, kuti: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake.”—Aroma 1:20.

N’zoona, Mulungu alikodi! Koma kodi akuloleranji kuti padziko lapansi pazichitika zinthu zomvetsa chisoni chonchi? Kodi ali n’cholinga chotani chodzachita padziko lapansi? Kodi tingadziŵe bwinobwino kuti Mulungu woona ndani?

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Ngati unaona mmene gudumu la ‘koloko’ limazungulirira—ungadziŵenso mmene magudumu enawo akuzungulirira, koma . . . usavutike ndi kuyankha funso lakuti anakunga sipiring’i ndani”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena