Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 7/8 tsamba 15
  • Kodi Wailesi Yakanema Njoopsa Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Wailesi Yakanema Njoopsa Motani?
  • Galamukani!—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Wailesi Yakanema Yakusinthani?
    Galamukani!—1991
  • Njira Zothandiza Kuti Musamaonere TV Kwambiri
    Galamukani!—2006
  • Kugwiritsa Ntchito Wailesi ya Kanema Mosamala Kwambiri
    Galamukani!—2000
  • Ilamulireni Wailesi Yakanema Isanakulamulireni
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 7/8 tsamba 15

Kodi Wailesi Yakanema Njoopsa Motani?

Pa December 18, 1997, nkhani za m’nyuzipepala zinati katuni ya pa wailesi yakanema inadwalitsa anthu ambiri ku Tokyo ku Japan. Mazanamazana anawatengera ku zipatala. “Ana ena anasanza magazi ndipo ena anadwala mwadzidzidzi kapena anakomoka,” inatero nyuzipepala ya The New York Times. “Madokotala ndi akatswiri a zamaganizo anachenjeza kuti zimene zachitikazi ndi chikumbutso chabwino cha mmene ana angakhalire pangozi chifukwa cha kuwonerera mafilimu ena a pa wailesi yakanema omwe alipo makono.”

New York Daily News inati: “Anthu a ku Japan anachita mantha dzulo pamene chinyama cha pa wailesi yakanema chinatong’ola maso ake ofiira ndipo ana mazanamazana anakomoka m’dziko lonse.

“Pafupifupi ana 600 ndiponso akulu oŵerengeka anakaŵagoneka m’zipinda zosamalira matenda adzidzidzi Lachiŵiri ataona . . . katuni pa wailesi yakanema.” Ena, omwe ankabanika, anakawagoneka m’zipinda za odwala ofunika chisamaliro chapadera.

Yukiko Iwasaki, mayi wa mwana wazaka zisanu ndi zitatu, anati: “Ndinadabwa kuona mwana wanga atakomoka. Anayamba kupuma pamene ndinammenya kumsana.”

Akonzi a maprogramu a ana pa wailesi yakanema analibe choti nkunena pa za chilombocho chimene iwo anati akhala akuchigwiritsira ntchito “nthaŵi zambiri” chinapangitsa bwanji zoopsazo.

Pozindikira kuopsa kwa kuonerera wailesi yakanema, makolo ena akhala akuyang’anira kuonerera wailesi yakanema mwina aletseratu kuionerera m’nyumba zawo. Kholo lina ku Allen, mu Texas, U.S.A, linati asanachotse wailesi yakanema m’nyumba mwawo, ana ake ankasonyeza kuti “sankakhala ndi chidwi ndi zinthu kwa nthaŵi yaitali, samachedwa kukwiya, sankagwirizanika, ndiponso ankanyansidwa kwambiri ndi zinthu zambiri.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Lerolino, pafupifupi aliyense wa ana athu asanu—amene ali ndi zaka zoyambira pa 6 mpaka 17—amapeza giredi A m’kalasi. Pamene anasiya kuonerera wailesi yakanema mwamsanga anayamba kuchita zinthu zina zowasangalatsa zonga maseŵera, kuŵerenga, zaluso, kugwiritsira ntchito kompyuta ndi zina zotero.

“Chinthu chimodzi chosaiŵalika chinachitika zaka ziŵiri zapitazo. Mwana wanga wamwamuna, amene panthaŵiyo anali ndi zaka zisanu nzinayi, ali kuphwando kwa mnzake kumene amafunika kuti agone komweko, anandiimbira foni, akumafuna kubwerera kunyumba . . . Nditapita kukamtenga ndi kumfunsa kuti chinavuta nchiyani, iye anati, ‘phwando silikusangalatsa. Zomwe akufuna kuchita ndi kungokhala nkumaonerera wailesi yakanema!’”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena