Kupsinjika Maganizo—“Wakupha Wachinsinsi”
“Chizindikiro choyamba chomwe ndinaona chinali kutopa kwambiri. Kunayambika pafupi ndi fupa lapachifuwa; kunakwera kufika pamapewa, khosi, ndi zibwano; ndiye nkutsikira mmanja anga. Zinkangokhala ngati kuti njovu yandiponda pachifuwa. Ndinkalephera kupuma. Ndinayamba kutuluka thukuta. Ndinayamba kumva kuwawa m’mimba ndiye kenaka kuchita mseru kwambiri. . . . Kenaka, pamene manesi anali kundigoneka pabedi lakuchipatala, ndikukumbukira ndikunena modabwa kuti, ‘Ndadwala mtima.’ Ndinali ndi zaka 44.”
DR. Robert S. Eliot analongosola motero mmene zinachitikira pamene anakhala pang’ono kufa zaka 20 zapitazo m’buku lake lotchedwa From Stress to Strength. M’maŵa tsiku lomwelo anali pamsonkhano ndipo analankhulapo—modabwitsanso za matenda a mtima. Mwadzidzidzi, Dr. Eliot, wodziŵa za matenda a mtima, anapezeka iye mwini ali pomwe akupatcha, “malo osayenera m’chipinda chothandizira odwala mtima.” Kodi nchiyani chimene iye akuona kuti chinapangitsa mavuto akewo? Dr. Eliot anati, “Chinkandipha ndi momwe ndinkachitira ndi kupsinjika maganizo kwanga.”a
Monga mmene zomwe anakumana nazo Dr. Eliot zikusonyezera, kupsinjika maganizo kumakhala ndi zotsatirapo zoopsa. Ndipotu, ku United States kwapezeka kuti ichi ndi chimodzi cha zinthu zakupha kwambiri. Zotsatira za kupsinjika maganizo zikhoza kumangokula pang’onopang’ono ndipo mkupita kwa nthaŵi nkudzaonekera mwadzidzidzi. Ndi zifukwa zabwino, kupsinjika maganizo kumatchedwa kuti “Wakupha Wachinsinsi.”
Chodabwitsa nchakuti, amene umunthu wawo ndi wagulu la A—okhala ndi khalidwe la kusadekha, chiwawa, ndi a mpikisano—sindiwo okha amene ali pangozi yokumana ndi mavuto odza chifukwa chopsinjika maganizo. Ngakhale amene khalidwe lawo ndi lofatsa nawonso alinso pangozi, makamaka amene kufatsa kwawo nkwapamaso chabe, ndipo kumangokhala ngati chivindikiriro chosagwiritsitsa pamphika wa maungu. Malinga nzimene zinamchitikira Dr. Eliot anapeza kuti zimenezi ndi zoona. Tsopano amachenjeza ena kuti: “Mukhoza kufa mwadzidzidzi—osadziŵa kuti ngoziyo mumayenda nayo nthaŵi zonse itamangiriridwa kumtima wanu.”
Koma matenda a mtima ndiponso imfa yamwadzidzidzi sindiwo mavuto okha okhudzana ndi kupsinjika maganizo, monga mmene nkhani yotsatirayi ikusonyezera.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti kupsinjika maganizo ndi chimodzi mwa zomwe zimapangitsa matenda a mtima, nzoonekeratu kuti matendawo amakhalapo makamaka mitsempha yopititsa magazi kumtima ikatsekeka ndi mafuta. Choncho nkosayenera kutenga zizindikiro za matenda a mtima mwachibwana, kapena kulingalira kuti kungosiya kukhala wopsinjika maganizo kudzakuchiritsani. Onani Galamukani! ya December 8, 1996, masamba 15-25.