Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 11/8 tsamba 22
  • Kodi Nchiyani Chimapatsa Anthu Chimwemwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimapatsa Anthu Chimwemwe?
  • Galamukani!—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Chimwemwe Chowona Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kufunafuna Moyo Wachimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 11/8 tsamba 22

Kodi Nchiyani Chimapatsa Anthu Chimwemwe?

Pazaka makumi aŵiri gulu la ofufuza padziko lonse lakhala likufufuza za chimwemwe mwatsatanetsatane. Kodi anapeza zotani? “Zikuoneka kuti chimwemwe kwenikweni sichimadalira pa zinthu zakunja,” inatero magazini ya Scientific American.

Magazini ya sayansi imeneyi inanenanso kuti: “Chuma sindicho umboni wakuti munthu ali wachimwemwe. Anthu sanakhale ndi chimwemwe chochuluka pamene maiko awo atukuka kwambiri. . . . M’maiko ambiri palibe kugwirizana kwenikweni pakati pa ndalama ndi chimwemwe.”

Zofufuzazo zikusonyeza kuti pali mikhalidwe inayi imene anthu achimwemwe ali nayo: Amadzikonda ndipo amadziŵerengera, amakhulupirira kuti ali ndi ulamuliro pa moyo wawo, samataya mtima, ndipo amakonda kucheza ndi anthu anzawo. Ndiponso, maukwati abwino ndi maunansi abwino ndi ena zimathandizira chimwemwe m’moyo, ndipo zimenezo zimalimbitsa thanzi ndi kuwonjezera moyo wa munthu.

Zili bwinonso kudziŵa zimene Scientific American inanena kuti: “Anthu opembedza kwambiri alinso ndi chimwemwe chochuluka. Pambuyo pa kufufuza kotchedwa Gallup kofuna kudziŵa zolingalira za anthu kunapezeka kuti anthu opembedza kwambiri amakhala ndi chimwemwe chachikulu kuposa aja amene saali odzipereka kwambiri pa zauzimu. Kufufuza kwina, kuphatikizapo kwa maiko 16 ogwirizana, pa anthu 166,000 m’maiko 14, kunapeza kuti malinga ndi malipoti, chimwemwe ndiponso kukhutira ndi moyo zimawonjezeka ngati pali kudzipereka zolimba pa chipembedzo ndi kusaphonya mapemphero.”

Kalekale wamasalmo Davide anasonyeza kuti chimwemwe cha munthu chimakhalapo ngati pali kulambira Yehova Mulungu kogwirizana, nalemba kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Salmo 122:1.

Nzosadabwitsa kuti mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: ‘Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi’! (Ahebri 10:24, 25) Inde, kusonkhana pamodzi ndi aja amene ali ndi chikhulupiriro chofanana ndi chathu polambira Mulungu kumasangalatsa amene amakonda choonadi cha Baibulo. Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zatsimikiza kuti zimenezi nzoona ndipo zikukupemphani kuti mudzadzionere nokha mwa kulambira nawo limodzi pa Nyumba ya Ufumu pafupi ndi kwanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena