Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 10/8 tsamba 32
  • Zomwe Matrakiti a Baibulo Angakwaniritse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Matrakiti a Baibulo Angakwaniritse
  • Galamukani!—1997
Galamukani!—1997
g97 10/8 tsamba 32

Zomwe Matrakiti a Baibulo Angakwaniritse

Mumzinda wa Golitsino, kufupi ndi Moscow, Russia, mmodzi wa Mboni za Yehova anapereka trakiti lakuti Sangalalani ndi Moyo Wabanja kwa mayi yemwe ankakankha chikuku. Mboniyo inapitiriza ndi ulendo wake, komabe posapita nthaŵi anamva liwu la mayiyo akuitana. Anali kumthamangira kuti ampeze, koma ali kukankha chikuku chija.

Mayiyo anati anali kufuna kuphunzira zambiri, motero Mboniyo inampatsa matrakiti ena aŵiri onena za nkhani zina za m’Baibulo. Inampatsanso nambala yake ya telefoni kuti adzathe kulankhula naye pambuyo pake. Usiku womwewo anaimba telefoni ndipo anapanga makonzedwe kuti azikhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba mlungu uliwonse. Mkati mwa miyezi isanu ndi iŵiri yokha, onse iye ndi mng’ono wake anadzipatulira kutumikira Mulungu ndipo anabatizidwa.

Ngati mukufuna kuŵerenga matrakiti a Baibulo akuti Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? ndi Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena kukeyala yoyenera ili patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena