Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 7/8 tsamba 32
  • “Sindinakonde Kuŵerenga Galamukani!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sindinakonde Kuŵerenga Galamukani!”
  • Galamukani!—1997
Galamukani!—1997
g97 7/8 tsamba 32

“Sindinakonde Kuŵerenga Galamukani!”

Amenewo ndiwo mawu a wophunzira wina pa Yunivesite ya San Jose State ku California, yemwe akuchita kosi ya Maphunziro a Malo Okhala. Akupitiriza kuti: “Ndinaganiza kuti magaziniyo ikanandilalikira kuti:—‘Pita kutchalitchi’ kapena, ‘Khala Mboni ya Yehova.’ Koma pamene ndinaŵerenga kope limeneli (January 8, 1996, ‘Pulaneti Lathu Lokhala Pangozi—Kodi Lingapulumutsidwe?’), ndinadabwa kupeza kuti inali ndi zenizeni! Nkhani zake zikuphatikizapo mapu a ‘Zovuta Zina za Malo Okhala a Padziko Lonse,’ amene akusonyeza malo kumene thengo lapululidwa kwambiri, zinyalala zapoizoni, kuipitsa mpweya, kusoŵa kwa madzi, zamoyo zimene zili pangozi ya kusoloka, ndi kuwononga nthaka.

“Mpaka pano sindinakhale ndi ana, komabe ndikudera nkhaŵa zoti kaya adzakhala nawo mpweya wabwino wopuma, mapaki oseŵereramo, kapena madzi oti azimwa. . . . Ndikukuyamikirani chifukwa cha nkhani zimenezi.”

Galamukani! tsopano imatuluka makope mamiliyoni 18.3 m’zinenero 80, zokwanira 56 zimafalitsidwa nthaŵi imodzi ndi Chingelezi. Ngati mungakonde kumaŵerenga magazini imeneyi nthaŵi zonse, chonde lankhulani ndi Mboni za Yehova za kwanuko, pafoni kapena ku Nyumba ya Ufumu yakonko, kapena kuwalembera pakeyala yapafupi ndi kwanu imene ili patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena