Nzeru ya Kupeŵa Kugonana ndi ya Kukwatirana ndi Munthu Mmodzi Yekha
LEROLINO, anthu ngati 30 miliyoni atenga kachilombo ka AIDS ndipo oposa 6 miliyoni afa. Tsiku lililonse anthu 8,500 atsopano amapezeka ndi kachilomboko—mwa amenewo, 1,400 ndi ana, amene kaŵirikaŵiri amafa m’chaka choyamba. Makampeni ophunzitsa anthu za kugonana kumene amati nkotetezereka agalamutsa anthu, komabe ena akuti zimenezo sizokwanira. Dr. Steven J. Sainsbury analemba m’magazini ya The Tampa Tribune, kuti “AIDS ndi nthenda yakupha, ndipo njira iliyonse yofuna kudzichinjiriza nayo iyenera kukhala yogwira ntchito mokwaniratu.”
Ponena za kugwiritsira ntchito makondomu kuchinjiriza AIDS, Dr. Sainsbury anati: “Tiyeni tione nkhaniyo mwa njira iyi. Tinene kuti, pachifukwa chosadziŵika, magalimoto angophulika pamene munthu akufuna kuliza injini. Oyendetsa magalimoto akuphulitsidwa kulikonse m’dziko. Potsirizira pake, boma likupeza njira yothetsera vutolo. Akunena kuti, tangoikani mankhwalaŵa m’mafuta a galimoto, ndipo ngozi za kuphulika kwa galimoto zidzachepa ndi 90 peresenti. Kodi mudzati vutolo latha? Kodi mudzapitiriza kuyendetsa galimoto lanu? Ndikukayikira. Nanga nchifukwa ninji tikuvomereza kuti makondomu ndiwo mankhwala othetsera AIDS?”
Poona kuti AIDS kaŵirikaŵiri imadza mwakugonana, Dr. Sainsbury akupereka mankhwala aŵa: “Peŵani kugonana kufikira mutaloŵa ukwati ndi munthu mmodzi wopanda matendawo. Mawu aakulu ndi akuti peŵani kugonana ndi akuti loŵani ukwati ndi munthu mmodzi yekha.”
Baibulo limalamula anthu osakwatira kupeŵa kugonana ndipo okwatira kukhala mu ukwati ndi munthu mmodzi yekha. Miyezo yapamwamba ya Baibulo imaletsa dama, chigololo, ndi kugonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. (Mateyu 19:4-6; 1 Akorinto 6:9, 10; 7:8, 9) Ngakhale kuti ambiri amatsutsa muyezo umenewu, namati sugwiranso ntchito kapena ngwachikale, khalidwe limene Baibulo limaphunzitsa lathandiza anthu kukhala ndi thanzi ndi mtendere wa maganizo.—Yesaya 48:17.