“Ntchito Yaikulu kwa Anthu”
“Mwachitira anthu ntchito yaikulu pofalitsa buku limeneli. Nlodabwitsa. Lolinganizidwa bwino koposa. Loyenera chiyamiko.
“Ubwino wake wa bukuli ngwakuti likukhudza mbali iliyonse yachipembedzo, ndipo pomatero munali osamala kuti musakhale osuliza. Ayi ntchito mwagwira. Nlopambanadi.”
Kodi munthu wophunzira kwambiri ameneyu wa ku Tiruchchirappalli, ku India, yemwe analemba kalata imeneyi, anali kunena za buku liti? Mankind’s Search for God, buku la masamba 384 la ziyambi ndi ziphunzitso za zipembedzo zazikulu zadziko—Chihindu, Chibuda, Chitaoizimu, Chikonfyushiani, Chishinto, Chiyuda, Chikristu, ndi Chisilamu. Mitu yotsirizira ikufotokoza za kusakhulupirira kwa makono ndi kutembenukiranso kwa Mulungu woona. Makope oposa 16 miliyoni a buku limeneli asindikizidwa m’zinenero 37.
Munthu wophunzirayo anali ataŵerenga buku lobwereka. Ndiye anafuna lakelake. Ngati mungakonde kulipenda nokha buku lokhalanso ndi zithunzi limeneli, chonde onanani ndi Mboni za Yehova m’dera lanu kapena lemberani ku keyala yapafupi ili patsamba 5 la magazini ano.