Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 2/8 tsamba 32
  • Anasonkhezeredwa ndi Chiyamikiro cha Serosha cha Galamukani!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anasonkhezeredwa ndi Chiyamikiro cha Serosha cha Galamukani!
  • Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 2/8 tsamba 32

Anasonkhezeredwa ndi Chiyamikiro cha Serosha cha Galamukani!

Wachichepere wina wakuboma la Washington, U.S.A., analemba kuti: “M’kalasi lophunzira Chingelezi tinayenera kulemba kalata ku magazini kapena ku nyuzipepala. Motero ndinayamba kufunafuna nkhani za m’magazini zimene ndingayankhe.

“Ndinasankha kuona nkhani za m’magazini a Galamukani! amene anabwera papositi dzulo. Ndili wachimwemwe kwambiri kuti ndinatero. Nkhani yakuti ‘Ulendo Wobwereza wa ku Russia,’ ya mu kope la March 8, 1995, inali yolimbikitsa kwambiri. Kunali kolimbikitsa makamaka kuŵerenga za changu cha Ufumu wa Mulungu cha Serosha wazaka zisanu ndi ziŵiri. Chikondi chake ndi chiyamikiro chake pa magazini a Galamukani! zinandichititsa kuganiza za nkhani za mu Galamukani! zimene sindinaŵerenge. Tsopano ndidzayamba kuyesetsa kwambiri kuŵerenga nkhani zonse zabwino za mu Galamukani! ndi Nsanja ya Olonda yomwe.”

Ngati mungafune kope la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena ngati mungakonde kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena