“Sindidzatayanso Makope Ena Ndisanawaŵerenge”
Mwamuna wina analembera afalitsi a Galamukani! akumalongosola kuti: “Posachedwapa ndinapeza kope la Galamukani! wa April 8, 1994 pakhomo panga. Iii! Kodi nchiyani chimene chachitika? Mwakonzadi magazini okhala ndi chidziŵitso chamakono a m’ma ‘90.’ Ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene nkhani zake zinayambira, ndipo ndinaŵerengadi nkhanizo kwa nthaŵi yoyamba. (Kaŵirikaŵiri ndinkaganiza kuti, ‘Aa, anthu aja anali panonso,’ ndi kutaya magaziniwo.) Mmenemo munali kanthu kena ka aliyense.”
Potsiriza pake iye analemba kuti: “Mwatenga njira yolondola. Pitirizani kuchita ntchito yabwinoyo, ndipo ndikukuuzitsani kuti sindidzatayanso makope ena ndisanawaŵerenge.”
Ngati mungakonde kuti kopa la Galamukani! litumizidwe kunyumba kwanu kapena mufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Pamwamba: Chilolezo cha ROE/Anglo-Australian Observatory, chithunzi cha David Malin