Tsamba 2
Kwa nthaŵi yaitali anthu azizwitsidwa ndi lingaliro la moyo wokhala kunja kwa dziko lapansi. Kuyambira pa chipangizo chamagetsi chakale cha mu 1899 (pamwamba kulamanja) kufikira maradio telescope aakulu (zipangizo zowonera kutali za mphamvu ya wailesi) (pansi) zimene zinagwiritsiridwa ntchito choyamba mu 1957 kufikira ku zofufuzira mlengalenga zapamwamba zonga ngati Viking (pamwamba kulamanzere) ya mu 1976, pakhala kuyesayesa kopitirizabe kwa kupeza moyo kunja kwa thambo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chithunzi chozikidwa pa NASA photo