Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 11/8 tsamba 21
  • Zimene Mwana Wosabadwa Amadziŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mwana Wosabadwa Amadziŵa
  • Galamukani!—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Makolo, Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kukhala ndi Pakati kwa Azaka Zapakati pa 13 ndi 19 Kodi Msungwana Angachitenji?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 11/8 tsamba 21

Zimene Mwana Wosabadwa Amadziŵa

KUFUFUZA kwaposachedwapa kukutsimikizira kuti mluza wosabadwa umayambukiridwa ndi zochulukira kwambiri kuposa chakudya cha mayiyo, mankhwala amene angagwiritsire ntchito, kapena kaya ngati amasuta kapena ayi. Mluzawo umamvanso zimene mayi wake amamvetserako ndipo motsimikizirika umayambukiridwa.

Kuti tichitire chitsanzo: Dairekitala wa nyimbo wa Hamilton Philharmonic Orchestra mu Ontario, Canada, anasimba kuti pamene anali wachichepere, unyinji wosiyanasiyana wa nyimbo zimene ankaziphunzira unawoneka kukhala wozoloŵereka mwachilendo, ngakhale kuti anali asanaziwonepo nkalelonse. Nthaŵi zonse inali mbali ya cello yomwe inali yozoloŵereka mwachinsinsi. Iye anauza amake, omwe anali katswiri wa cello, ponena za izi. Pamene mwanayo anafunsidwa ndi mayi wake ndipo anauza mayiyo maina a nyimbo zomwe ankaziphunzira, chinsinsicho chinathetsedwa. Iye analongosola kuti, pamene anali ndi pakati pa mwanayo, zimenezi ndizo nyimbo zenizeni zomwe ankaziphunzira!

Tsopano, mogwirizana ndi wolemba nkhani za m’nyuzipepala Erma Bombeck, magazine a mankhwala a ku Britain akusimba ponena za vuto limene magazinewo akulitcha “kumwerekera ku zosatsa malonda kwa mluza.” Ana osabadwa akukhala omwerekera ku maprogramu osatsa malonda a pa TV amene mayi wawo amamvetserako. “Ndikulakalaka kuti nkadadziŵa izi pamene ndinkanyamula ana anga,” analongosola choncho Bombeck. “Bwenzi ndinkawonerera ‘The Waltons,’” programu ya wailesi ya kanema yomangirira ya zaka zingapo zapitazo. Iye anawonjezera kuti: “Nchosadabwitsa kuti tikukhala ndi ana omwe amafuna kuti makutu awo abooledwe pa msinkhu wa zaka 2, kupita kocheza pamene ali ndi zaka 9 ndi kukhala ndi nyumba yawoyawo pa msinkhu wa zaka 13.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena