Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 11/8 tsamba 15
  • Kuchilikizidwa ndi Chiyembekezo cha Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchilikizidwa ndi Chiyembekezo cha Ufumu
  • Galamukani!—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Wandidalitsa Kwambiri Chifukwa cha Zimene Ndinasankha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • “Ndasunga Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kufesa Mbewu za Choonadi cha Ufumu
    Nsanja ya Olonda—2000
Galamukani!—1989
g89 11/8 tsamba 15

Kuchilikizidwa ndi Chiyembekezo cha Ufumu

MU APRIL 1987 Lila, mkazi yemwe ali m’zaka zake za m’ma 80, anawonerera mwamuna wake akumwalira m’chipatala pafupi ndi Portland, Oregon. Maso a anamwino achifundowo anali pa mkaziyo. Anayang’ana mtembowo ndipo kenaka anatsanzika ndi kuwukhudza.

“Munali mwamuna wabwino kwambiri,” iye anatero. “Ndidzakuwonani m’chiukiriro!” Kenaka anatembenuka ndi kunena kuti: “Ndanena zimenezo chifukwa ndine m’modzi wa Mboni za Yehova. Lolani kuti ndilongosole.” Iye anapitiriza kulongosola za chiukiriro ndi dziko latsopano la Mulungu.

Pambuyo pake, pamene ankachoka pa chipatalapo, katswiri wa matenda a mtima amene ankasamalira mwamuna wake anakumana naye m’kanjira ka mkatimo kopitamo. Anaima ndi kulongosola chisoni chake. Panthaŵi yomweyo mkaziyo anayamba kulongosola kuti posachedwapa adzamuwona mwamuna wake m’dziko latsopano kupyolera mwa chiukiriro. Anapereka umboni wokwanira dokotalayo asananyamuke, akumati: “Lila, ndikhulupirira zidzachitika motero kwa iwe.” Pamene ankatembenuka kuti adzipita, Lila ananena kuti: “Zidzatero, ndipo ndikufuna kudzakuwona iwenso m’menemo!”

Mosadziwika kwa Lila, dokotalayo anafikiridwa ndi Mboni za Yehova. Tsopano, powona mmene chikhulupiriro cha Lila chinamulimbikitsira mkati mwa kupsyinjika ndi imfa ya mwamuna wake ndi kumva kawonedwe kake kotsimikiza kaamba ka chiyembekezo cha mtsogolo, dokotalayo analimbikitsidwa. Iye limodzi ndi mkazi wake anapitiriza kukambitsirana kwawo ndi Mboni za Yehova.

Miyezi ingapo pambuyo pake, mu January 1988, Lila anayamba kudwala ndipo anathera m’chipatala. Mankhwala sanali kugwira ntchito pa iye ndipo matendawo ankaipiraipirabe. Katswiri wa matenda a mtima uja anamva ponena za icho ndipo mwamsanga anapita kukamuchezera m’chipinda cha odwalitsa. Iye anafunsa kuti: “Kodi uli bwanji Lila?”

“Osati bwino kwenikweni.”

“Ukumulakalaka Erick, kodi sichoncho?”

“Inde, ndikhulupirira tero, kuposa ndi kalelonse.”

Kenaka analankhula naye ponena za lonjezo la Baibulo lonena za kudzamuwonanso Erick m’chiukiriro, limodzinso ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya wangwiro m’dziko latsopano. Kwenikwenidi, izi ndizo zinthu zenizeni zimene Lila anamuuza poyambirirapo pamene mwamuna wake anamwalira! Anali mankhwala abwino koposa amene adakampatsa. Anapeza bwino, natuluka m’chipatala mkati mwa mlunguwo, ndipo anayambanso uminisitala Wachikristu ndi nyonga yatsopano.

Ndipo bwanji ponena za katswiri wa matenda a mtimayo? Iye ndi mkazi wake anapereka miyoyo yawo kwa Mulungu ndipo anabatizidwa pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mu Corvallis, Oregon, mu June 1988.—Yoperekedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena