Tsamba 2
Kusuta kapena kusasuta, limenelo ndilo funso. Ilo kaŵirikaŵiri limayang’anizidwa pamene muli a zaka za pakati pa 13 ndi 19. Palibe thayo lophatikizidwamo. Chiri chosankha cha chikhumbo chomasuka. Koma mogwirizana ndi maulamuliro a zamankhwala, chiri chosankha chimene chingakhale ndi ziyambukiro zowopsya m’moyo wanu. Icho chingagamulepo pamene ndi mmene mungafere.
Chotero, mafunso ofunika kwambiri amadzutsidwa: Kodi chiri chabwino kusatsa malonda a zopangidwa za fodya? Kodi chiri cholungamitsidwa mwa makhalidwe kaamba ka mitundu yotchedwa Yachikristu kugulitsa kunja zopangidwa zawo za fodya, kuziika izo pa maiko ena? Kodi ogulitsa ndudu akugulitsa matenda ndi imfa? Ndipo popeza kuti anthu amasankha kusuta, kodi icho chiridi kanthu kwenikweni?