Tsamba 2
Kukongola, kusiyanasiyana, ndi kapangidwe m’chilengedwe kamatsogolera ambiri kukhulupirira kuti payenera kukhala Mlengi wa nzeru. Komabe, kwa ena ambiri, chokhumudwitsa chachikulu cha kukhulupirira kwawo mwa Mulungu kuli kukhalapo kwa kuvutika ndi kuipa m’dziko. Ngati ‘Mulungu ali wachikondi,’ nchifukwa ninji iye amalola zinthu zoipa zambiri chotero kuchitika kwa anthu abwino? Kodi pali zifukwa zenizeni kwa Mulungu za kulolera kuipa? Kodi pali chifukwa chirichonse cha kukhulupirira kuti zoipa zidzatha mtsogolo moyandikira?