Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt 2 Peter 1:1-3:18
  • 2 Petulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Petulo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Petulo

KALATA YACHIWIRI YA PETULO

1 Ndine Simoni Petulo, kapolo komanso mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulembera anthu amene apeza chikhulupiriro chamtengo wapatali chofanana ndi chathu kudzera mʼchilungamo cha Mulungu wathu ndiponso cha Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

2 Kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndi mtendere wake ziwonjezereke kwa inu. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kudziwa molondola+ Mulungu komanso Yesu Ambuye wathu. 3 Pogwiritsa ntchito mphamvu yake, Mulungu watipatsa kwaulere zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo komanso kuti tikhale odzipereka kwa iye. Zimenezi zatheka chifukwa chodziwa molondola za Mulungu amene anatiitana+ kudzera mu ulemerero ndi ubwino wake. 4 Kudzera mʼzinthu zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mogwirizana ndi malonjezo amenewa mukhale ndi ulemerero umene Mulungu ali nawo.+ Wachita zimenezi chifukwa tinasiya kuchita makhalidwe oipa amʼdzikoli amene amayamba chifukwa cholakalaka zinthu zoipa.

5 Chifukwa cha zimenezi, yesetsani mwakhama+ kuwonjezera makhalidwe abwino+ pa chikhulupiriro chanu, pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu,+ 6 pa kudziwa zinthu kudziletsa,+ pa kudziletsa kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu,+ 7 pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.+ 8 Mukamachita zinthu zonsezi komanso mukamasonyeza kwambiri makhalidwewa, mudzagwiritsa ntchito zinthu zimene mukuzidziwa molondola zokhudza Ambuye wathu Yesu Khristu ndipo zidzakuthandizani kuti musamangokhala kapena kulephera kubereka zipatso.+

9 Munthu amene alibe makhalidwe amenewa ndi wakhungu, watseka maso ake kuti asaone kuwala+ ndipo waiwala kuti anayeretsedwa ku machimo+ omwe ankachita kalekale. 10 Choncho abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, nʼcholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana+ ndi kuwasankha. Mukapitiriza kuchita zimenezi, simudzalephera ngakhale pangʼono.+ 11 Ndipotu mudzadalitsidwa kwambiri moti mudzalowa mwaulemerero mu Ufumu wosatha+ wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+

12 Pa chifukwa chimenechi, ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba mʼchoonadi chimene munaphunzira. 13 Choncho ndikuona kuti ndi bwino kuti ndizikugwedezani pokukumbutsani zimenezi+ pamene ndidakali mʼthupi langali, lomwe lili ngati msasa.*+ 14 Ndikuona choncho chifukwa ndikudziwa kuti ndatsala pangʼono kutuluka mumsasa wangawu, mogwirizana ndi mmene Ambuye wathu Yesu Khristu anandiuzira.+ 15 Nthawi zonse ndiziyesetsa kukukumbutsani kuti ndikadzachoka muzidzatha kukumbukira nokha zinthu zimenezi.

16 Pamene tinkakudziwitsani za mphamvu za Ambuye wathu Yesu Khristu komanso zokhudza kukhalapo* kwake, sitinatengere nkhani zabodza zimene anthu amapeka mochenjera. Koma tinakuuzani zinthu zokhudza ulemerero wake zimene tinachita kuona ndi maso athu.+ 17 Chifukwa Khristu analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu, Atate wathu, pamene mawu anamveka kwa iye kuchokera mu ulemerero waukulu kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene amandisangalatsa kwambiri.”+ 18 Tinamva mawu amenewa kuchokera kumwamba pamene tinali naye limodzi mʼphiri loyera.

19 Nʼchifukwa chake sitikayikira ngakhale pangʼono kuti mawu aulosiwa adzakwaniritsidwa ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewa aziwala mʼmitima yanu ngati nyale+ imene ikuwala mumdima. Pitirizani kuchita zimenezi mpaka mʼbandakucha, nthanda*+ itatuluka. 20 Inu mukudziwa mfundo yofunika yakuti, palibe ulosi wa mʼMalemba umene umachokera mʼmaganizo a munthu. 21 Chifukwa ulosi sunachokere kwa anthu,+ koma anthuwo analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa* ndi mzimu woyera.+

2 Komabe pakati pa Aisiraeli, anthu ena anakhala aneneri abodza.* Mofanana ndi zimenezi pakati panu padzakhalanso aphunzitsi abodza.*+ Anthu amenewa adzayambitsa mwachinsinsi timagulu towononga tampatuko ndipo adzakana ngakhale Ambuye wawo amene anawagula.+ Chifukwa chochita zimenezi, iwo adzawonongedwa mofulumira kwambiri. 2 Kuwonjezera pamenepo, ambiri adzatengera khalidwe lopanda manyazi*+ la aphunzitsi abodzawo ndipo anthu azidzalankhula monyoza njira ya choonadi chifukwa cha aphunzitsiwo.+ 3 Komanso mwadyera azidzagwiritsa ntchito mawu achinyengo nʼcholinga choti akudyereni masuku pamutu. Koma chilango chimene Mulungu anakonza kalelo kuti adzawapatse,+ chikubwera mofulumira ndipo chiwonongeko chawo chidzafika ndithu.+

4 Ndipotu Mulungu sanalekerere angelo amene anachimwa aja+ osawapatsa chilango. Koma anawaponya mu Tatalasi,*+ anawamanga mumdima wandiweyani podikira kuti adzawaweruze.+ 5 Mulungu sanalekerere dziko lakale lija osalipatsa chilango,+ koma anasunga Nowa, yemwe ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.+ Anamupulumutsa limodzi ndi anthu enanso 7,+ pamene anabweretsa chigumula padziko la anthu osaopa Mulungu.+ 6 Anawononganso mizinda ya Sodomu ndi Gomora poitentha ndi moto.+ Anachita zimenezi kuti likhale chenjezo kwa anthu osaopa Mulungu la zimene zidzawachitikire mʼtsogolo.+ 7 Koma anapulumutsa Loti yemwe anali munthu wolungama.+ Loti ankavutika kwambiri mumtima chifukwa cha khalidwe lopanda manyazi* limene anthu ophwanya malamulo ankachita. 8 (Munthu wolungamayu ankavutika mumtima tsiku ndi tsiku chifukwa cha zimene ankaona ndiponso kumva pamene ankakhala pakati pa anthu oipa. Iye ankavutika mumtima chifukwa cha zochita zawo zosamvera malamulo.) 9 Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova* amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.+ Koma anthu osalungama amawasunga kuti adzawawononge pa tsiku lopereka chiweruzo,+ 10 makamaka anthu amene amafunafuna anthu ena nʼcholinga choti awaipitse pogonana nawo+ ndiponso amene amanyoza olamulira.+

Anthu amenewa saopa chilichonse komanso amamva zawo zokha. Iwo sachita mantha kulankhula zinthu zonyoza anthu amene Mulungu wawapatsa ulemerero. 11 Koma angelo, ngakhale kuti ndi amphamvu kwambiri, saneneza aphunzitsi abodzawo ndi mawu onyoza, chifukwa angelowo amalemekeza Yehova.*+ 12 Ndipo anthu amenewa, mofanana ndi nyama zopanda nzeru zimene zimangochita zinthu mwachibadwa komanso zimabadwa kuti zidzagwidwe ndi kuwonongedwa, amalankhula monyoza za zinthu zimene sakuzidziwa.+ Anthu amenewa adzawonongedwa chifukwa cha zochita zawo zoipa, 13 ndipo akukumana ndi mavuto monga mphoto ya zochita zawo zoipa.

Iwo amaona kuti kuchita zinthu zimene amalakalaka nʼkosangalatsa,+ ngakhale atamazichita masana. Anthu amenewa ali ngati mawanga ndi litsiro lothimbirira pakati panu, ndipo amasangalala mopitirira malire akamakuphunzitsani zinthu zabodza pamene akudya nanu limodzi.+ 14 Amalakalaka kwambiri kuchita chigololo*+ komanso amalephera kupewa tchimo, ndipo amakopa anthu achikhulupiriro chosalimba. Ali ndi mtima wophunzitsidwa dyera. Iwo ndi ana otembereredwa. 15 Asocheretsedwa chifukwa anasiya njira yowongoka. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anachita zinthu zoipa chifukwa chofunitsitsa kulandira mphoto,+ 16 koma anadzudzulidwa chifukwa cholephera kuchita zinthu zabwino.+ Bulu amene salankhula, analankhula ngati munthu nʼkulepheretsa zochita zamisala za mneneriyo.+

17 Amenewa ndi akasupe opanda madzi komanso nkhungu yotengeka ndi mphepo yamkuntho, ndipo anawasungira mdima wandiweyani.+ 18 Amalankhula mawu odzitukumula opanda pake. Ndipo amagwiritsa ntchito zilakolako za thupi+ komanso khalidwe lopanda manyazi* pokopa anthu amene angothawa kumene kwa anthu ochita zoipa.+ 19 Ngakhale kuti akuwalonjeza ufulu, eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa.+ Chifukwa aliyense amene wagonjetsedwa ndi winawake, amakhala kapolo wa womugonjetsayo.*+ 20 Ndithudi, ngati anapulumuka ku zodetsa za dzikoli+ chifukwa chodziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, koma nʼkuyambiranso kuchita zinthu zomwe zija mpaka kugonjetsedwa nazo, makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.+ 21 Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njira ya chilungamo, kusiyana nʼkuidziwa bwinobwino kenako nʼkupatuka pa malamulo oyera omwe analandira.+ 22 Mwambi woona uja wakwaniritsidwa pa iwo. Mwambiwo umati: “Galu wabwerera kumasanzi ake, ndipo nkhumba imene inasambitsidwa yapita kukagubudukanso mʼmatope.”+

3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yachiwiri imene ndikukulemberani, ndipo mofanana ndi yoyamba ija, ndikukulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito bwino mphamvu zanu zoganiza pokukumbutsani zimene mukudziwa kale.+ 2 Ndikuchita zimenezi kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kalero komanso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu anapereka kudzera mwa atumwi.* 3 Choyamba dziwani kuti mʼmasiku otsiriza kudzakhala anthu amene azidzalankhula zinthu zonyoza. Potsatira zinthu zimene amalakalaka,+ 4 azidzati: “Kodi kukhalapo* kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti?+ Taonani, palibe chimene chasintha kungochokera tsiku limene makolo athu anamwalira. Zinthu zonse zikupitiriza kuchitika ndendende ngati mmene zakhala zikuchitikira kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.”+

5 Anthu amenewa amanyalanyaza mwadala mfundo yakuti, kalero panali kumwamba ndi dziko lapansi lomwe linatuluka mʼmadzi ndi kuima pamwamba pa madziwo chifukwa cha mawu a Mulungu.+ 6 Ndipo kudzera mʼzinthu zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamira mʼmadzi a chigumula.+ 7 Koma ndi mawu a Mulungu omwewo, kumwamba ndi dziko lapansi zimene zilipo panopa, azisungira moto ndipo akuzisungabe mpaka pa tsiku limene adzaweruze komanso kuwononga anthu osaopa Mulungu.+

8 Komabe okondedwa, musalephere kuzindikira mfundo yakuti, kwa Yehova* tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi.+ 9 Yehova* sakuchedwa kukwaniritsa zimene analonjeza+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa. Koma akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.+ 10 Komabe, tsiku la Yehova*+ lidzafika ngati wakuba,+ pamene kumwamba kudzachoka+ ndi mkokomo waukulu. Ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka, moti dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.+

11 Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka chonchi, ganizirani za mtundu wa anthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. 12 Muzichita zimenezi pamene mukuyembekezera komanso kukumbukira nthawi zonse* kubwera kwa tsiku la Yehova.*+ Pa tsikuli kumwamba kudzapsa ndi moto nʼkuwonongekeratu+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka. 13 Koma pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake,+ ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.+

14 Choncho okondedwa, popeza mukuyembekezera zinthu zimenezi, yesetsani kuchita zonse zimene mungathe kuti Mulungu adzakupezeni muli oyera, opanda cholakwa ndiponso muli mumtendere.+ 15 Kuwonjezera pamenepo, muziona kuti kuleza mtima kwa Ambuye wathu ndi chipulumutso, monganso mmene mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberani mogwirizana ndi nzeru zimene anapatsidwa.+ 16 Iye anafotokoza zimenezi ngati mmene amachitira mʼmakalata ake onse. Komabe mʼmakalata akewo muli zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osaphunzitsika komanso achikhulupiriro chosalimba akuzipotoza. Amachita zimenezi ngati mmene amachitiranso ndi Malemba ena onse, zomwe zidzachititse kuti adzawonongedwe.

17 Choncho inu okondedwa, popeza mwadziwiratu zimenezi, chenjerani kuti anthu ophwanya malamulowo asakusocheretseni ndi zochita zawo zoipa nʼkuchititsa kuti mugwe chifukwa cholephera kukhala olimba.+ 18 Musatero ayi, koma muzichita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mupitirize kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, ndiponso kuti mumudziwe bwino kwambiri. Kwa iye kukhale ulemerero, kuyambira panopa mpaka muyaya. Ame.

Mawuwa amatanthauza malo amene munthu akukhala mongoyembekezera ndipo Petulo anawagwiritsa ntchito mophiphiritsa ponena za thupi lake.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pangʼono kutuluka.

Mʼchilankhulo choyambirira, “motengedwa; mokankhidwa.”

Kapena kuti, “aneneri onyenga.”

Kapena kuti, “aphunzitsi onyenga.”

Kapena kuti “adzatengera zochita zawo zosonyeza khalidwe lopanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Maso awo ndi odzaza ndi chigololo.”

Kapena kuti, “komanso zochita zawo zosonyeza khalidwe lopanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “amene wagonjetsedwa ndi chinachake, amakhala kapolo wa chinthucho.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “atumwi anu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “komanso kufunitsitsa.”

Onani Zakumapeto A5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena